Konzekelani Kudzakhala ndi Moyo m’Dziko Latsopano
“Uwalamule kuti azicita zabwino, . . . kuti agwile mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 TIM. 6:18, 19.
1, 2. (a) Ndi madalitso otani akuthupi amene tikuyembekezela m’Paladaiso? (Onani cithunzi pamwambapa.) (b) Nanga tikuyembekezela madalitso otani akuuzimu?
AMBILI a ife tikamva mau akuti “moyo weniweniwo,” timaganizila za ciyembekezo ca moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi. Mtumwi Paulo anafananitsa mau akuti “moyo wosatha” ndi akuti “moyo weniweniwo”. (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:12, 19.) Tikuyembekezela moyo wosatha umene udzatipangitsa kukhala okhutila ndi osangalala. N’zovuta kufotokoza mmene tizidzamvelela kuuka tsiku lililonse tili ndi thanzi labwino, mtima uli m’malo, ndiponso tilibe nkhawa iliyonse. (Yes. 35: 5, 6) Ganizilani mmene tidzasangalalile kuceza ndi acibale, anzathu, kuphatikizapo amene adzaukitsidwa. (Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15) Tidzakhalanso ndi mwayi wodziŵa zambili za cilengedwe, kuonjezela luso lathu loimba, zomangamanga ndi zinthu zina zambili.
2 Tidzasangalala kwambili ndi zinthu zabwino zimene tinalonjezedwa, koma madalitso aakulu amene tidzalandila ndi akuuzimu. Tidzasangalala kuona dzina la Yehova litayeletsedwa ndiponso kuona Ufumu wake ukulamulila cilengedwe conse. (Mat. 6:9, 10) Tidzasangalalanso kwambili kuona colinga ca Yehova cakuti anthu adzadze dziko lapansi cikukwanilitsidwa. Ndipo cidzakhala copepuka kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova popeza mwapang’onopang’ono tidzayamba kukhala angwilo.—Sal. 73:28; Yak. 4:8
3. Kodi tiyenela kukonzekela ciani?
3 Sitikaikila kuti madalitso onsewa tidzawapeza cifukwa cakuti Yesu anati: “zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Mat. 19:25, 26) Koma kuti tidzakhalebe ndi moyo ngakhale pambuyo pa ulamulilo wa zaka 1000 wa Yesu, tiyenela kucitapo kanthu tsopano kuti ‘tigwile mwamphamvu’ moyo wosatha. Conco pamene tikuyembekezela mapeto a dziko loipali tiyeni tiyesetse kukhala ndi makhalidwe abwino. Tikatelo ndiye kuti tikukonzekela kudzakhala m’dziko latsopano. Kodi tingacite bwanji zimenezi popeza tili m’dongosolo lino loipa la zinthu?
MMENE TINGAKONZEKELELE
4. Fotokozani citsanzo ca mmene tingadzikonzekeletsele kudzakhala m’dziko latsopano.
4 Kodi tingakonzekele bwanji kudzakhala m’dziko latsopano la Mulungu? Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti mukufuna kupita ku dziko lina. Kodi mungakonzekele bwanji? Coyamba, mungayambe kuphunzila cinenelo ndi cikhalidwe ca anthu a kudzikolo. Mungadziŵiletu zakudya zakumeneko. Mungayambe kucita zinthu ngati kuti muli kale ku dziko limenelo. Ndipo kucita zimenezo n’kofunika cifukwa ndi mmene moyo wanu udzakhalile kudzikolo. Mofananamo, ifenso tifunika kukonzekela tsopano mwa kukhala ndi makhalidwe amene adzatithandize kudzakhala m’dziko latsopano. Conco, tiyeni tikambilane mmene tingacitile zimenezi.
5, 6. Kodi kumvela malangizo amene timapatsidwa masiku ano kungatithandize bwanji kukonzekela dziko la tsopano?
5 Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila dziko lonse m’dziko la tsopano. Kulamulilidwa ndi Mulungu kudzakhala kosangalatsa cifukwa kudzasiyana ndi maulamulilo a anthu osonkhezeledwa ndi Satana. Olamulila m’dzikoli amacita zinthu mwadyela ndipo amaumilila maganizo ao, io akana kutsogoleledwa ndi Mulungu. Zimenezi zacititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambili, cisoni, ndi masoka. (Yer. 10:23) Tikuyembekezela mwacidwi nthawi imene anthu onse adzagonjela kuulamulilo wa Yehova.
6 M’dziko latsopano, tidzakhala okondwa kuyendela malangizo a Yehova pogwila nchito yokongoletsa dzikoli, kuphunzitsa oukitsidwa, ndi kucita cifunilo ca Yehova. Nanga bwanji ngati panthawiyo tidzapemphedwa kugwila nchito inayake imene siitisangalatsa? Kodi tidzamvela malangizo ndi kugwila nchitoyo mwakhama ndiponso mosangalala? Ambili aife tinganene kuti inde. Cabwino, koma kodi masiku ano timamvela malangizo amene timapatsidwa? Ngati timatelo, ndiye kuti tikukonzekela kudzakhala ndi moyo wamuyaya m’dziko lolamulidwa ndi Yehova.
7, 8. (a) N’cifukwa ciani tifunika kukhala ogwilizanika? (b) Kodi Akristu ena akumana ndi masinthidwe otani? (c) Kodi ndife otsimikiza kuti moyo udzakhala bwanji m’dziko latsopano?
7 Tingakonzekele kudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano mwa kugonjela makonzedwe a Yehova masiku ano. Koma tifunikanso kuyesetsa kukhala okhutila ndiponso ogwilizanika. Ngati timamvela amene akutitsogolela mwa kukhala okhutila ndi osangalala ndi utumiki uliwonse umene tapatsidwa ndiye kuti m’dziko latsopano tidzaonetsanso khalidwe limenelo. (Ŵelengani Aheberi 13:17.) M’Dziko Lolonjezedwa, Aisiraeli anali kupatsidwa colowa malinga ndi kuculuka kwa anthu. (Num. 26:52-56; Yos. 14:1, 2) Masiku ano, sitidziŵa kumene tidzauzidwa kukakhala m’dziko latsopano. Koma kugonjela kudzatithandiza kukhala okhutila ndiponso osangalala pamene tikucita cifunilo ca Yehova kulikonse kumene tidzakhale panthawiyo m’dziko latsopano.
8 Ngati timagwilizana ndi gulu la Yehova ndi kusamalila maudindo amene tapatsidwa, ndiye kuti ndife oyenelela kudzakhala mu Ufumu wa Mulungu. N’zoona kuti m’kupita kwa nthawi zinthu zikhoza kusintha paumoyo wathu. Mwacitsanzo, a m’banja la Beteli ena ku United States anawapatsa mautumiki ena ndi kuwatumiza m’mipingo ndipo adalitsidwa kwambili m’mautumiki ena a nthawi zonse. Atumiki oyendela ena anasinthidwa kukhala apainiya apadela cifukwa ca ukalamba kapena zinthu zina. Ngati timayesetsa kukhala okhutila, kupempha thandizo kwa Yehova, ndi kucita zomwe tingathe mu utumiki wake, tidzakhala osangalala ndipo tidzalandila madalitso ambili ngakhale tikukhala m’masiku otsiliza. (Ŵelengani Miyambo 10:22.) Nanga bwanji za madalitso amene tiyembekezela mtsogolo? Mwina timaganizila za malo ena m’dziko latsopano amene tingakonde kudzakhalako, koma tingadzapemphedwe kukhala malo ena. Mosasamala kanthu za kumene tidzatumikila kapena zimene tidzacita, ndife otsimikiza kuti tidzakhala oyamikila, okhutila, ndiponso osangalala kwambili.—Neh. 8:10.
9, 10. (a) Ndi panthawi iti pamene tidzafunika kuonetsa kuleza mtima m’dziko latsopano? (b) Tingaonetse bwanji kuti ndife oleza mtima?
9 M’dziko latsopano, padzakhala nthawi zina pamene tidzafunika kuonetsa kuleza mtima. Mwacitsanzo, tingadzamve za anthu ena amene aukitsidwa, ndipo anzao ndi acibale ao akusangalala. Komabe mwina ife tingadzafunike kuyembekezela kwa kanthawi kuti okondedwa athu aukitsidwe. Zitadzacitika conco, kodi tingadzaonetse kuleza mtima ndi kusangalala ndi anzathu? (Aroma 12:15) Kuyesetsa kukhala oleza mtima tsopano pamene tikuyembekezela kukwanilitsidwa kwa malonjezo a Yehova kudzatithandiza kuti tidzakhale oleza mtima mtsogolo.—Mlal. 7:8.
10 Tingakonzekelenso kudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano mwa kukhala oleza mtima pamene kamvedwe kathu ka coonadi kasintha. Kodi timakonda kuŵelenga ndi kukhala oleza mtima pamene coonadi ca m’Baibulo cikumveketsedwa pang’onopang’ono? Ngati timatelo, ndiye kuti sicidzakhala covuta kugonjela m’dziko latsopano pamene Yehova azidzadziŵitsa mtundu wa anthu zimene amafuna.—Miy. 4:18; Yoh. 16:12.
11. Kodi panthawi ino Yehova akutiphunzitsa ciani pa nkhani ya kukhululuka? Nanga zimenezo zidzatipindulitsa bwanji m’dziko latsopano?
11 Khalidwe lina limene tifunika kukhala nalo pamene tikukonzekela kudzakhala m’dziko latsopano ndi mzimu wokhululuka. Mu Ulamulilo wa Kristu wa Zaka 1000, mwina zidzatenga nthawi kuti olungama ndi osalungama akhale angwilo. (Mac. 24:15) Kodi panthawiyo tizidzacitilana zinthu mwacikondi? Ngati tiyesetsa kukhululukilana masiku ano ndi kukhala paubwenzi wabwino ndi ena, sicidzakhala covuta kucita zimenezi panthawiyo.—Ŵelengani Akolose 3:12-14.
12. Fotokozani kugwilizana kumene kulipo pakati pa moyo wa mtsogolo ndi mmene tiyenela kukhalila masiku ano.
12 Kukhala ndi moyo m’dziko latsopano sikutanthauza kuti tidzakhala ndi ciliconse cimene tafuna panthawiyo. Koma mulimonse mmene zinthu zidzakhalile tidzafunika kukhala oyamikila ndiponso okhutila pamene tikugonjela ku ulamulilo wabwino wa Yehova. Tidzafunika kusonyeza makhalidwe amene Yehova akutiphunzitsa tsopano. Pamene tiyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino timaonetsa kuti takonzekela kudzakhala m’dziko latsopano kwamuyaya. (Aheb. 2:5; 11:1) Ndiponso timaonetsa kuti tikufuna kukhala m’dziko limene anthu onse azidzamvela Yehova.
IKANI MAGANIZO ANU PA ZINTHU ZAKUUZIMU
13. Ndi zinthu ziti zimene zidzakhala zofunika kwambili m’dziko latsopano?
13 Tiyeni tikambilanenso njila ina imene tingakonzekelele kudzakhala ndi moyo weniweni umene ukubwela. Ngakhale kuti tinalonjezedwa zakudya zambili ndi zinthu zina zabwino m’dziko latsopano, tidzasangalalanso kwambili pamene zosowa zathu zakuuzimu zidzakhutilitsidwa. (Mat. 5:3) Kucita zinthu za kuuzimu ndi cinthu cacikulu cimene tizidzacita m’dziko latsopano ndipo tidzaonetsa kuti tikusangalala kwambili mwa Yehova. (Sal. 37:4) Ngati tiika zinthu za kuuzimu pa malo oyamba m’moyo wathu, ndiye kuti tikukonzekela kudzakhala ndi moyo weniweni mtsogolo.—Ŵelengani Mateyu 6:19-21.
14. Ndi zolinga za kuuzimu ziti zimene zingathandize acinyamata kukhala ndi moyo weniweni m’maganizo?
14 Kodi tingacite ciani kuti tizikonda kwambili zinthu za kuuzimu? Njila imodzi ndi mwa kukhala ndi zolinga za kuuzimu. Ngati ndinu wacinyamata ndipo mukufuna kucita zambili muutumiki wa Yehova, yesetsani kuŵelenga zofalitsa zathu zimene zili ndi nkhani zofotokoza mautumiki osiyanasiyana a nthawi zonse ndipo sankhani umodzi mwa mautumiki amenewa kuti ukhale colinga canu. * Ndiponso muziceza ndi ena amene akhala muutumiki wa nthawi zonse kwanthawi yaitali. Mukamatumikila Yehova ndi moyo wanu wonse mudzakhala ndi maluso amene adzakuthandizani kutumikila Yehova m’dziko latsopano.
15. Ndi zolinga ziti zimene alengezi a Ufumu angakhale nazo?
15 Monga alengezi a Ufumu, ndi zolinga za kuuzimu ziti zimene tingakhale nazo? Tingadziikile zolinga monga kunola luso lathu m’mbali zina za utumiki. Kapena tingayesetse kumvetsa mfundo za m’Baibulo ndi kuona mmene zingatithandizile paumoyo wathu. Bwanji mutayesetsa kukulitsa luso lanu lokamba nkhani ndi kuŵelenga pa gulu kapena kupeleka mayankho pa misonkhano? Mungaganizilenso zolinga zina zimene mungakwanitse. Mfundo yaikulu ndi yakuti: Kukhala ndi zolinga za kuuzimu kudzakucititsani kukonda kwambili zinthu za kuuzimu zimene zidzakuthandizani kukonzekela kudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano.
TINAYAMBA KALE KULANDILA MADALITSO
16. N’cifukwa ciani kutumikila Yehova ndiye njila yabwino koposa?
16 Kodi kugwilitsila nchito nthawi yathu kukonzekela kudzakhala m’dziko latsopano la Mulungu, kutanthauza kuti tiyenela kunyalanyaza zinthu zina zimene zingatithandize kukhala okhutila masiku ano? Iyai. Ngati pali cinthu cimene tingacite kuti tikhale ndi moyo wokhutila, ndi kutumikila Yehova. Koma sikuti tifunika kucita zimenezi mwa mwambo cabe kuti tikapulumuke pa cisautso cacikulu. Kutumikila Yehova ndiye njila yabwino imene tingapezelemo cimwemwe. Kutsogoleledwa ndi Yehova, ndiponso kukhala m’cikondi cake cosatha ndi cinthu cabwino kwambili kuposa cina ciliconse. (Ŵelengani Salimo 63:1-3.) Komabe, sikuti tifunika kuyembekezela dziko latsopano kuti tikasangalale ndi madalitso akuuzimu amene amabwela cifukwa cotumikila Yehova ndi mtima wonse. Ngakhale panopa tikhoza kusangalala cifukwa madalitso amenewo tili nao. Ena a inu mwakhala mukusangalala ndi madalitso amenewo kwa zaka zambili, ndipo malinga ndi zimene taona tikuvomeleza kuti palibe njila ina yamoyo imene ingabweletse cimwemwe.—Sal. 1:1-3; Yes. 58:13, 14.
17. Kuti tikapitilizebe kusangalala ndi zimene timakonda m’dziko latsopano, kodi tidzafunika kuika ciani pa malo oyamba?
17 M’dziko latsopano la Mulungu tidzakhalanso ndi nthawi yosangalala ndi zinthu zimene timakonda. Yehova anatilenga m’njila yakuti tizisangalala, n’cifukwa cake akutilonjeza kuti ‘adzakhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.’ (Sal. 145:16. Mlal. 2:24) Timafuna kusangalala ndi kupumula, koma ngati tiika ubwenzi wathu ndi Yehova pa malo oyamba timasangalala kwambili ndi zinthu zimenezi. Ndi mmenenso zidzakhalila m’dziko latsopano. Conco ndi cinthu canzelu kupitilizabe “kufunafuna ufumu coyamba” ndi kuika maganizo athu pa madalitso amene timalandila cifukwa cotumikila Yehova.—Mat. 6:33.
18. Tingaonetse bwanji kuti tikukonzekela kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso?
18 M’dziko latsopano limene likubwelali tidzasangalala kwambili kuposa mmene timasangalalila masiku ano. Tingaonetse kuti tikufunitsitsa kudzakhala ndi moyo weniweni mwa kukonzekela tsopano. Tiyeni tikhale ndi makhalidwe amene Mulungu amafuna ndi kugwila mwakhama nchito imene tapatsidwa yolalikila za Ufumu. Komanso, tiyeni tizisangalala cifukwa coika zinthu za Ufumu pamalo oyamba. Popeza tili ndi cikhulupililo colimba m’malonjezo a Yehova, tiyeni tikonzekele kudzakhala m’dziko latsopano.
^ par. 14 Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiŵili, masamba 311 mpaka 318.