Yehova Adzakucilikizani
“Yehova adzacilikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.”—SALIMO 41:3.
1, 2. Kodi Mulungu anacita ciani m’nthawi zakale? Nanga anthu ena masiku ano amaganiza ciani akadwala?
NGATI munadwalapo mwakayakaya, mwina munadzifunsapo kuti, ‘Mwati ine ndidzacila?’ Mwina mnzanu kapena wacibale wanu akudwala, ndipo mukudela nkhawa kuti kaya adzacila kapena ai. Mwacibabwa, anthufe timafuna kukhala ndi thanzi labwino, ndipo timafunanso kuti anthu amene timakonda akhale ndi thanzi labwino. M’Baibulo timaŵelenga za anthu ena amene anali kudwala ndipo anafuna kudziŵa ngati adzacila. Mwacitsanzo, Mfumu Ahaziya, mwana wa Ahabu ndi Yezebeli, anali kufuna kudziŵa ngati cilonda cake cidzapola. Patapita nthawi, nayenso Mfumu Benihadadi wa ku Siriya atadwala, anali kufuna kudziŵa ngati adzacila.—2 Mafumu 1:2; 8:7, 8.
2 Baibulo limatiuzanso kuti kale, Yehova nthawi zina anali kucilitsa anthu mozizwitsa ndi kuukitsa akufa kudzela mwa aneneli ake. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:17-20, 32-35) Masiku ano, anthu odwala amafunanso kudziŵa ngati Mulungu adzacitapo kanthu kuti awacilitse.
3-5. Kodi Yehova ndi Yesu ali ndi mphamvu yocita ciani? Nanga tikambilana mafunso ati?
Genesis 12:17; Numeri 12:9, 10; 2 Samueli 24:15) Yehova analanganso Aisiraeli ndi “milili” cifukwa ca kusakhulupilika kwao. (Deuteronomo 28:58-61) Panthawi ina, Yehova anateteza anthu ake ku matenda. (Ekisodo 23:25; Deuteronomo 7:15) Ena anawacilitsa. Mwacitsanzo, iye anacilitsa Yobu amene anali kudwala kwambili cakuti anali kufuna cabe kufa.—Yobu 2:7; 3:11-13; 42:10, 16.
3 Yehova ali ndi mphamvu yocita zinthu zimene zingakhudze thanzi la munthu. Kale, iye analanga anthu ena mwa kuwadwalitsa. Anacita zimenezi kwa anthu monga Farao wa m’nthawi ya Aburahamu ndiponso Miriamu mlongosi wa Mose. (4 Sitikaikila kuti Yehova ali ndi mphamvu yocilitsa odwala. Yesu nayenso ali ndi mphamvu yocilitsa odwala. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anacilitsa anthu odwala matenda monga khate ndi khunyu. Anacilitsanso anthu osaona ndi ofa ziwalo. (Ŵelengani Mateyu 4:23, 24; Yohane 9:1-7) Tikamaganizila zozizwitsa zimenezi, timayembekezela mwacidwi zinthu zosangalatsa zimene Yesu adzacita m’dziko latsopano. Ndipo panthawiyo, “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti ndikudwala.”—Yesaya 33:24.
5 Ngati mwadwala kwambili, kodi muyenela kuyembekezela kuti Yehova kapena Yesu adzakucilitsani mozizwitsa? Nanga tiyenela kuganizila ciani posankha cithandizo ca mankhwala?
MUZIDALILA YEHOVA MUKADWALA
6. N’ciani cimene Baibulo limakamba ponena za zozizwitsa zimene Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kucita?
6 M’nthawi ya atumwi, Yehova anadzoza Akristu ndi mzimu wake woyela. Ndipo ena anawapatsa mphamvu yocita zozizwitsa. (Machitidwe 3:2-7; 9:36-42) Mwacitsanzo, io anali kucilitsa anthu ndi kukamba zinenelo zosiyanasiyana. (1 Akorinto 12:4-11) Koma patapita nthawi, kucita zozizwitsa kunatha monga mmene Baibulo limakambila. (1 Akorinto 13:8) Conco, masiku ano sitiyenela kuyembekezela kuti Mulungu adzaticilitsa kapena kucilitsa okondedwa athu mozizwitsa.
Yehova amadziŵa bwino mavuto amene atumiki ake akukumana nao, ndipo saiŵala kukhulupilika kwao
7. Kodi lemba la Salimo 41:3 lingatilimbikitse bwanji?
7 Ngakhale n’conco, mukadwala, Yehova adzakulimbikitsani ndi kukucilikizani monga mmene anacitila kwa atumiki ake akale. Mfumu Davide analemba kuti: “Wodala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka. Patsiku latsoka Yehova adzamupulumutsa. Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.” (Salimo 41:1, 2) Apa Davide sanatanthauze kuti munthu wabwino amene amaganizila munthu wonyozeka sangafe. Nanga kodi Yehova akanathandiza bwanji munthu wabwinoyo? Davide anafotokoza kuti: ‘Yehova adzamucilikiza pamene akudwala pabedi lake. Adzamusamalila bwino kwambili pamene akudwala.’ (Salimo 41:3) Yehova amadziŵa bwino mavuto amene atumiki ake amakumana nao. Iye saiŵala atumiki ake. Angawapatse mphamvu ndi nzelu. Ndiponso Yehova analenga thupi la munthu m’njila yakuti lizitha kudzicilitsa.
8. Malinga ndi Salimo 41:4, n’ciani cimene Davide anapempha kwa Yehova pamene anadwala kwambili?
8 Pa Salimo 41, Davide anakambanso za nthawi pamene anadwala kwambili cakuti anada nkhawa ndi kufooka. Zioneka kuti pa nthawiyo Abisalomu mwana wake anafuna kumulanda Ufumu. Davide anali wodwala kwambili cakuti sanathe kulepheletsa ciwembu ca Abisalomu. Iye anadziŵa kuti chimo limene anacita ndi Batiseba ndi limene linabweletsa mavuto m’banja lake. (2 Samueli 12:7-14) Kodi Davide anacita ciani? Anapemphela kwa Yehova. Iye anati: “Inu Yehova ndikomeleni mtima, ndicilitseni pakuti ndakucimwilani.” (Salimo 41:4) Davide anadziŵa kuti Yehova anamukhululukila macimo ake ndipo anadalila Yehova pamene anali kudwala. Koma kodi Davide anali kufuna kuti Yehova amucilitse mozizwitsa?
9. (a) Kodi Yehova anamucitila ciani Hezekiya? (b) Kodi Davide anali kukhulupilila kuti Yehova amucitila ciani?
9 N’zoona kuti panthawi ina Mulungu anacilitsa anthu. Mwacitsanzo, pamene Mfumu Hezekiya anali pafupi kufa, Yehova anamucilitsa. Yehova anamuonjezela zaka zina 15. (2 Mafumu 20:1-6) Koma Davide sanayembekezele kuti Mulungu amucilitsa mozizwitsa. M’malomwake, anali kukhulupilila kuti Mulungu angamuthandize monga mmene angathandizile “munthu wocita zinthu moganizila munthu wonyozeka.” Davide anali paubwenzi wabwino ndi Yehova. Conco anapempha Yehova kuti amutonthoze ndi kumucilikiza pamene anali kudwala. Anapemphanso kuti amucilitse. Ifenso tingapemphe Yehova kuti atithandize monga mmene anathandizila Davide.—Salimo 103:3.
10. N’ciani cinacitikila Terofimo ndi Epafurodito? Nanga zimenezi zitiphunzitsa ciani?
10 M’nthawi ya atumwi, Paulo ndi ena anali ndi mphamvu yocilitsa odwala, koma si Akristu onse amene anacilitsidwa mozizwitsa. (Ŵelengani Machitidwe 14:8-10.) Mtumwi Paulo anacilitsa bambo wa Papuliyo amene anali kudwala malungo ndi kamwazi. Paulo ‘anapemphela ndipo anasanjika manja ake pa io ndi kuwacilitsa.’ (Machitidwe 28:8) Koma Paulo sanacilitse aliyense amene iye anali kudziŵa. Mmodzi wa mabwenzi a Paulo, Terofimo, anayenda naye limodzi paulendo wina waumishonale. (Machitidwe 20:3-5, 22; 21:29) Pamene Terofimo anadwala, Paulo sanamucilitse. Conco, Terofimo anatsalila ku Mileto kuti apezeko bwino. (2 Timoteyo 4:20) Mnzake wina, dzina lake Epafurodito, nayenso anadwala kwambili cakuti anatsala pang’ono kufa. Koma Baibulo silikamba kuti Paulo anamucilitsa.—Afilipi 2:25-27, 30.
KODI MUYENELA KUTSATILA MALANGIZO OTANI?
11, 12. N’ciani cimene tikudziŵa ponena za Luka? Nanga zioneka kuti iye anathandiza bwanji Paulo?
11 Luka anali dokotala ndipo anali kuyendela pamodzi ndi Paulo. (Machitidwe 16:10-12; 20:5, 6; Akolose 4:14) Iye ayenela kuti anali kuthandiza Paulo ndi anzake akadwala pamaulendo aumishonale. (Agalatiya 4:13) Izi zigwilizana ndi zimene Yesu anakamba kuti “odwala” amafuna dokotala.—Luka 5:31.
Tifunika kukhala osamala munthu wina akatipatsa malangizo okhudza thanzi lathu
12 Luka, sanali cabe munthu wokonda kupatsa anthu malangizo a zaumoyo. Iye anaphunzila za udokotala. Baibulo silikamba nthawi imene Luka anaphunzila za udokotala kapena kumene anaphunzilila. Koma limakamba kuti Luka anatumiza moni kwa Akristu a ku Kolose kupitila mwa Paulo. Conco, n’kutheka kuti Luka anaphunzila za udokotala ku Sukulu ya Zacipatala mumzinda wa Leodikaya, umene unali pafupi ndi mzinda wa Kolose. Ndiponso pamene Luka anali kulemba Buku la Uthenga Wabwino ndi la Machitidwe, anagwilitsila nchito mau oonetsa kuti analidi dokotala. Popeza anali dokotala, m’mabuku amene analemba, muli nkhani zambili zokhudza kucilitsa kumene Yesu anacita.
13. N’ciani cimene tiyenela kukumbukila tisanauze munthu malangizo okhudza thanzi kapena ifeyo tisanatsatile malangizo amene tapatsidwa?
13 Masiku ano, Akristu anzathu sangaticilitse mozizwitsa. Komabe, abale athu ena pofuna kutithandiza angatipatse malangizo okhudza thanzi ngakhale kuti sitinawapemphe. Malangizo ena amene angatipatse angakhale abwino. Mwacitsanzo, Paulo anauza Timoteyo kuti azimwako vinyo pang’ono. Timoteyo anali ndi vuto la m’mimba. Mwina vutoli linabwela cifukwa ca madzi oipa amene anali kumwa. * (Onani mau a munsi.) (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:23.) Komabe, tifunika kukhala osamala. Mkristu mnzathu angatiuze kuti timwe mankhwala ena ake a kucipatala kapena azitsamba. Angatiuzenso kuti tizidya kapena kupewa kudya zakudya zina. Iye angakambe kuti wacibale wake anali ndi vuto ngati lathu, ndipo anacila atacita zimenezo. Koma zimenezi sizitanthauza kuti ifenso tidzacila tikatsatila malangizowo. Tizikumbukila kuti mankhwala angathe kubweletsa mavuto aakulu ngakhale kuti anthu ambili amawagwilitsila nchito.—Ŵelengani Miyambo 27:12.
MUZIKHALA OSAMALA
14, 15. (a) Kodi tiyenela kusamala ndi anthu otani? (b) Kodi tikuphunzila ciani pa lemba la Miyambo 14:15?
14 Tonse timafuna kukhala ndi thanzi labwino kuti tizisangalala ndi umoyo ndiponso kuti tizitumikila bwino Yehova. Komabe, popeza ndife opanda ungwilo n’zosatheka kupewa matenda onse. Ngati tadwala pamakhala zithandizo za mankhwala zosiyanasiyana, ndipo tili ndi ufulu wosankha cithandizo cimene tifuna. Nthawi zina, anthu ndi makampani ena amakamba kuti apanga mankhwala ocilitsa matenda amene tikudwala. Koma amakamba zimenezi pofuna cabe kudyela anthu masuku pamutu. Iwo angakambe kuti anthu ambili amene anamwa mankhalawo anacila. Ndipo ngati, tikudwala timafuna kucita ciliconse cimene cingatithandize kuti ticile Miyambo 14:15.
ndi kukhala ndi moyo wautali. Koma sitiyenela kuiŵala malangizo a m’Baibulo akuti: “Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mau alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.”—Tifunika kukhala oganiza bwino ndi kupewa kukhulupilila zilizonse
15 Tiyenela kukhala ‘ocenjela’ ndiponso anzelu mwa kupewa kukhulupilila zilizonse zimene munthu angatiuze, makamaka ngati munthuyo sanaphunzile zacipatala. Tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Munthu uyu wakamba kuti cakudyaci kapena mankhalawa anathandiza anthu ena ake, koma kodi pali umboni wosonyeza kuti anawathandizadi? Ngati anawathandizadi, ndidziŵa bwanji kuti inenso adzandithandiza? Kodi ndiyenela kufufuza zina zowonjezeleka pankhaniyi ndi kukambitsilana ndi anthu amene anaphunzila za udokotala kuti andithandize?’—Deuteronomo 17:6.
16. N’ciani cimene tiyenela kuganizila tikamapanga zosankha zokhudza thanzi lathu?
16 Posankha njila zopimila matenda kapena cithandizo ca mankhwala, tiyenela kukhala ‘oganiza bwino’ ndi osamala. (Tito 2:12) Zimenezi n’zofunika kwambili makamaka ngati njila zopimila matenda kapena cithandizo ca mankhwala n’zokaikitsa. Kodi munthu amene mwafikila wakufotokozelani mmene adzakupimilani ndi mmene mankhwalawo amagwilila nchito? Kodi zimene wafotokoza zikumveka zacilendo? Kodi madokotala ambili avomeleza kuti njila yopimilayo kapena mankhwalawo angathandizedi? (Miyambo 22:29) Mwina munthu wina angakuuzeni kuti mankhwala ocilitsa matendawo apezeka kwinakwake kutali, koma madokotala akalibe kuwadziŵa. Koma kodi pali umboni wokwanila wosonyeza kuti mankhwala otelo aliko? Anthu ena angakupatseni mankhwala osadziŵika bwino kapena okhudzana ndi zamizimu. Kugwilitsila nchito mankhwala otelo n’koopsa. Musaiŵale kuti Mulungu amaticenjeza kuti tisamacite zamizimu kapena zamatsenga.—Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 1:13.
“TIKUFUNILANI ZABWINO ZONSE!”
17. Mwacibadwa, kodi anthufe timafuna ciani?
17 M’nthawi ya atumwi, bungwe lolamulila linatumiza kalata kwa abale m’mipingo yowadziŵitsa zinthu zina zimene anafunika kupewa. Kumapeto kwa kalatayo, bungwe lolamulila linalemba kuti: “Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambili, zinthu zidzakuyendelani bwino. Tikufunilani zabwino zonse!” (Machitidwe 15:29) Ngakhale kuti mau othela m’kalatayo anali njila ina yolailila, mauwa amatikumbutsa kuti mwacibadwa anthufe timafuna kukhala ndi thanzi labwino.
18, 19. Ndi umoyo wotani umene tikuyembekezela kudzakhala nao m’dziko latsopano?
18 Popeza ndife opanda ungwilo, sitingapewe matenda onse. Ndipo tikadwala, sitiyembekezela kuti Yehova aticilitsa mozizwitsa. Koma timayembekezela kuti mtsogolo Mulungu adzathetsa matenda onse. Pa Chivumbulutso 22:1, 2, mtumwi Paulo anakamba za “madzi a moyo” ndi “mitengo ya moyo” zimene zidzacilitsa anthu onse. Izi siziimila mankhwala azitsamba amene tingagwilitsile nchito panopa kapena m’dziko latsopano. M’malomwake, zimaimila zinthu zonse zimene Yehova ndi Yesu adzacita mtsogolo kuti tidzakhale ndi moyo wosatha.—Yesaya 35:5, 6.
19 Tikuyembekezela mwacidwi nthawi yabwino imeneyo. Koma pakali pano, tidziŵa kuti Yehova amatikonda, ndi kuti amadziŵa mmene timamvelela tikamavutika. Monga Davide, tili ndi cidalilo cakuti iye sadzatisiya tikadwala. Nthawi zonse, Yehova amasamalila anthu okhulupilika kwa iye.—Salimo 41:12.
^ par. 13 Buku lina linakamba kuti asayansi apeza kuti tuzilombo twa thaifodi ndi tuzilombo twina toyambitsa matenda, tumafa mwamsanga akatusakaniza ndi vinyo.—The Origins and Ancient History of Wine.