Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tumikilani Yehova Asanafike Masiku Oipa

Tumikilani Yehova Asanafike Masiku Oipa

“Kumbukila Mlengi wako Wamkulu.”—MLAL. 12:1.

1, 2. (a) Kodi Solomo anauzilidwa kulemba uphungu wotani kwa acinyamata? (b) N’cifukwa ciani Akristu a zaka za m’ma 50 kapena kuposelapo ayenelanso kucita cidwi ndi uphungu wa Solomo?

 MFUMU SOLOMO mouzilidwa analembela acinyamata kuti: “Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako, asanafike masiku oipa.” Kodi “masiku oipa” ndi ati? Solomo anagwilitsila nchito mau a ndakatulo ocititsa cidwi pofotokoza mavuto amene okalamba amakumana nao monga kunjenjemela manja, kuyenda mwapenda-penda, kuguluka manu, kusaona bwino, kuvutika kumva, imvi, ndi kuyenda moŵelama. Ndiye cifukwa cake Solomo anatiuza kuti tiyenela kukumbukila Mlengi wathu Wamkulu tikali acinyamata.—Ŵelengani Mlaliki 12:1-5.

2 Akristu ambili amene ali ndi zaka za m’ma 50 kapena kuposelapo akali amphamvu. N’zoona kuti angakhale ndi imvi, koma mwina thanzi lao silofooka kwambili monga mmene Solomo anafotokozela. Kodi Akristu acikulile amenewa angapindule bwanji ndi uphungu wouzilidwa wopita kwa acinyamata wakuti: “Kumbukila Mlengi wako Wamkulu”? Kodi uphungu umenewu umatanthauzanji?

3. Kodi kukumbukila Mlengi wathu Wamkulu kumaphatikizapo ciani?

3 Ngakhale kuti tatumikila Yehova kwa zaka zambili, ndi bwino kuti nthawi ndi nthawi tizisinkha-sinkha za ukulu wa Mlengi wathu. Moyo ndi mphatso yamtengo wapatali. Moyo umenewu unalengedwa m’njila yodabwitsa kwambili cakuti sitingathe kuumvetsetsa. Zinthu zosiyana-siyana zimene Yehova analenga n’zocititsa cidwi ndipo zimatipangitsa kusangalala ndi moyo m’njila zambili. Tikamasinkha-sinkha za cilengedwe ca Yehova, timakumbukila kuti iye ndi wacikondi, wanzelu ndiponso wamphamvu. (Sal. 143:5) Koma kukumbukila Mlengi wathu Wamkulu kumaphatikizapo kusinkha-sinkha zimene iye amafuna kwa ife. Kusinkha-sinkha zimenezi kumatipangitsa kuyamikila kwambili mlengi wathu ndi kum’tumikila mmene tingathele tikali moyo.—Mlal. 12:13.

MIPATA YAPADELA IMENE ACIKULILE ALI NAYO

4. Kodi Akristu amene atumikila kwa zaka zambili ayenela kudzifunsa funso liti? Ndipo n’cifukwa ciani?

4 Popeza kuti ndinu wacikulile, mosakaikila mumadziŵa zinthu zambili. Komabe muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndidzacita ciani ndi moyo wanga tsopano ndikaliko ndi mphamvu?’ Pokhala Mkristu wodziŵa zambili, muli ndi mwai umene ena alibe. Mwacitsanzo mungaphunzitseko acinyamata zinthu zimene mwaphunzila kwa Yehova. Mungalimbikitse ena mwa kuwasimbila zocitika zimene mwasangalala nazo potumikila Mulungu. Mfumu Davide anapempha mwai wocita zimenezi pamene analemba kuti: “Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambila pa unyamata wanga. . . . Ngakhale nditakalamba ndi kumela imvi, inu Mulungu musandisiye, kufikila nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatila, kufikila nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwela m’tsogolo.”—Sal. 71:17, 18

5. Kodi Akristu acikulile angathandize bwanji ena ndi cidziŵitso cao?

5 Kodi mungathandize bwanji ena ndi cidziŵitso cimene mwapeza cifukwa cotumikila kwa zaka zambili? Kodi mungaitanile atumiki acinyamata kunyumba kwanu kuti mukhale ndi maceza olimbikitsa? Kodi mungakonze zopita nao muulaliki kuti aone cimwemwe cimene muli naco cifukwa cotumikila Yehova? Munthu wakale Elihu anati: “Masiku alankhule. Zaka zambili n’zimene ziyenela kudziŵitsa anthu nzelu.” (Yobu 32:7) Mtumwi Paulo analangiza akazi acikulile acikristu kuti azilimbikitsa ena mwa mau ndi zocita. Iye ananena kuti: “Akazi acikulile . . . akhale aphunzitsi a zinthu zabwino.”—Tito 2:3.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUTHANDIZE ENA

6. N’cifukwa ciani Akristu amene atumikila zaka zambili ndi ofunika?

6 Ngati ndinu Mkristu amene mwatumikila kwa zaka zambili, pali zambili zimene mungacite kuti muthandize ena. Ganizilani zimene mukudziŵa tsopano poyelekezela ndi zimene munali kudziŵa zaka 30 kapena 40 zapitazo. Inu mumadziŵa bwino kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibo paumoyo wanu. Mosakaikila, mumatha kufika ena pamtima powaphunzitsa coonadi ca m’Baibo. Ngati ndinu mkulu, mumadziŵa mmene mungathandizile abale amene apatuka n’kuyamba kulowela njila yolakwika. (Agal. 6:1) Mwina mwaphunzila kuyang’anila nchito za mpingo, madipatimenti adela, kapena kumanga Nyumba za Ufumu. Mwaphunzilanso mmene mungalimbikitsile madokotala kucita maopaleshoni popanda kugwilitsila nchito magazi. Ngakhale kuti mwina munabatizika posacedwapa mumadziŵa zambili paumoyo. Mwacitsanzo, ngati muli ndi ana, muli ndi nzelu zothandiza kwambili. Akristu acikulile ali ndi luso lofunika pothandiza anthu a Yehova mwa kuphunzitsa, kutsogolela, ndi kulimbikitsa abale ndi alongo.—Ŵelengani Yobu 12:12.

7. Kodi Akristu acikulile angawaphunzitse ciani acinyamata?

7 Kodi cidziŵitso cimene muli naco mungacigwilitsile nchito bwanji mokwanila? Mwina mungathandize acinyamata mmene angayambitsile ndi kutsogozela maphunzilo a Baibo. Ngati ndinu mlongo, kodi mungathandize makolo acitsikana kukhalabe olimba mwakuuzimu ngakhale kuti akusamalila ana? Ngati ndinu m’bale, kodi mungaphunzitse abale acinyamata mmene angapelekele nkhani zolimbikitsa ndi kukhala alaliki ogwila mtima a uthenga wabwino? Kodi mungasonyeze acinyamata mmene angalimbikitsile abale ndi alongo acikulile mwakuuzimu? Ngakhale kuti muli ndi mphamvu zocepelapo tsopano, mukali ndi mwai waukulu wophunzitsa acinyamata. Mau a Mulungu amati: “Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zao, ndipo ulemelelo wa anthu okalamba ndiwo imvi zao.”—Miy. 20:29.

KUTUMIKILA KU MALO OSOŴA

8. Kodi mtumwi Paulo anacita ciani pamene anali wacikulile?

8 Mtumwi Paulo anatangwanika kwambili muutumiki wa Yehova pamene anali wacikulile. Panthawi imene anamasulidwa m’ndende ku Roma ca m’ma 61 C.E., Paulo anali atagwila nchito yake ya umishonale mwakhama ndi kupilila mayeselo ambili. Mwina iye akanasankha kukhala ku Roma kuti azilalikila kumeneko. (2 Akor. 11:23-27) Ndipo abale a mumzinda waukulu umenewu akanakonda kuti akhale naye kumeneko kuti aziwalimbikitsa. Koma Paulo anazindikila kuti kumaiko ena kunali kusoŵa kwakukulu. Conco, anapanga ulendo wina wa umishonale. Paulendowo iye anatenga Timoteyo ndi Tito ndi kupita nao ku Efeso, kenako ku Kerete ndipo mwina anakafika ku Makedoniya. (1 Tim. 1:3; Tito 1:5) Sitidziŵa ngati anafika ku Spain, koma anali ndi colinga copita kumeneko.—Aroma 15:24, 28.

9. Kodi zikuoneka kuti ndi liti pamene Petulo anasamukila kumalo osoŵa? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

9 Mtumwi Petulo ayenela kuti anali ndi zaka zoposa 50 pamene anapita kumalo osoŵa. Tidziŵa bwanji zimenezo? Ngati anali ndi zaka zakubadwa zofanana ndi Yesu kapena kuposelapo pang’ono, ndiye kuti pamene anakumana ndi atumwi ena ku Yerusalemu mu 49 C.E anali ndi zaka pafupi-fupi 50. (Mac. 15:7) Pambuyo pa msonkhanowo, Petulo anapita kukakhala ku Babulo. Mosakaikila colinga cake cinali kukalalikila Ayuda ambili amene anali kukhala mumzindawo. (Agal. 2:9) Ali kumeneko ca m’ma 62 C.E., ndi pamene anauzilidwa kulemba kalata yake yoyamba. (1 Pet. 5:13) Kukhala ku dziko lina kungakhale kovuta, koma Petulo sanalole ukalamba kumulepheletsa kupeza cimwemwe cifukwa cotumikila Yehova mokwanila.

10, 11. Kodi Robert ndi mkazi wake anacita ciani pamene anali ndi zaka za m’ma 50?

10 Masiku ano, Akristu ambili a zaka za m’ma 50 kapena kuposelapo amaona kuti umoyo wao wasintha ndi kuti angatumikile Yehova m’njila zina. Ena amapita kukatumikila kumalo osoŵa. Mwacitsanzo, Robert anati: “Ine ndi mkazi wanga tinali ndi zaka pafupi-fupi 55 pamene tinaona kuti tili ndi mipata yambili yotumikila Yehova. Mwana wathu mmodzi yekha anali atacoka panyumba ndipo makolo athu anali atamwalila. Tinalinso ndi ndalama zocepa zimene makolo athu anasiya. Nditaŵelengela mtengo ndinaona kuti zingakhale bwino kugulitsa nyumba kuti tilipile loni, ndiyeno ndalama zotsala zingatithandize pa zosoŵa zathu kufikila nditatenga penshoni. Tinamva kuti anthu ambili ku Bolivia anali kufunitsitsa kuphunzila Baibo, ndipo umoyo kumeneko unali wosalila zambili. Conco tinaganiza zosamukila kumeneko. Zinali zovuta kuti tizoloŵele umoyo watsopano cifukwa zinthu kumeneko zinali zosiyana poyelekeza ndi ku North America. Koma tinadalitsidwa cifukwa ca khama lathu.”

11 Robert akupitiliza kuti: “Cinthu cofunika kwambili paumoyo wathu tsopano ndi kugwila nchito zampingo. Anthu ena amene tinali kuphunzila nao Baibo anabatizidwa. Banja lina limene tinali kuphunzila nalo Baibo limakhala kutali kumudzi wina wosauka kwambili. Koma io amayenda mtunda wamakilomita angapo mlungu uliwonse kucoka kumudzi kubwela kutauni kudzasonkhana. Timasangalala kwambili kuona banja limeneli likupita patsogolo. Ndipo mwana wao wamkulu wamwamuna anayamba upainiya.”

KUTHANDIZA M’MAGAWO OLANKHULA CINENELO CINA

12, 13. Fotokozani cocitika ca Mkristu wina amene anapeza njila zina zotumikila Yehova atapuma pa nchito.

12 Mipingo ya zinenelo zina kapena tumagulu ingapindule kwambili ndi citsanzo ca abale ndi alongo acikulile. Komanso kutumikila m’magawo amenewo kumakhala kosangalatsa. Mwacitsanzo, Brian wa ku Britain analemba kuti: “Nditafika zaka 65 ndinapuma pa nchito, ndipo izi zinacititsa kuti umoyo ukhale wosasangalatsa. Ana athu anali atacoka pakhomo, ndipo kunali kovuta kupeza anthu acidwi kuti tiphunzile nao Baibo. Ndiyeno ndinakumana ndi mnyamata wacichaina amene anali kufufuza zinazake pa yunivesite kudela lathu. Iye anavomela kubwela ku misonkhano yathu, ndipo ndinayamba kuphunzila naye Baibo. Pambuyo pa milungu ingapo, iye anayamba kubwela ndi bwenzi lake la cichaina kumisonkhano. Pambuyo pa milungu iŵili anabwelanso ndi anzake aŵili. Conco onse pamodzi ndi iye anakwana anai.”

13 “Pamene bwenzi lake lacisanu linapempha kuti ndiziphunzila nalo Baibo, ndinaona kuti ngakhale kuti ndili ndi zaka 65 sindiyenela kusiya kutumikila Yehova. Conco, ndinapempha mkazi wanga amene ali ndi zaka 63 kuti tiphunzile cinenelo ca Cichaina. Pophunzila cineneloci tinali kugwilitsila nchito matepu. Papita zaka 10 kucokela pamene tinaphunzila Cichaina. Kulalikila m’gawo la cinenelo cina kunaticititsa kudzimva monga takhalanso acinyamata. Pakali pano taphunzila Baibo ndi anthu a Cichaina okwana 112. Ambili a io amafika pamisonkhano ndipo mmodzi amatumikila nafe monga mpainiya.”

SANGALALANI MWA KUCITA ZIMENE MUNGATHE

14. Kodi Akristu acikulile ayenela kusangalala ndi ciani? Nanga citsanzo ca Paulo cingawalimbikitse bwanji?

14 Ngakhale kuti Akristu ambili a zaka za m’ma 50 ali ndi mipata yocita zinthu zina zatsopano muutumiki wa Yehova, ena samakwanitsa kutelo. Ena amadwala-dwala, ena amasamalila makolo ao okalamba kapena ana amasiye. Koma simuyenela kuiwala kuti Yehova amayamikila zilizonse zimene mumacita pom’tumikila. Conco, mmalo mokhumudwa cifukwa colephela kucita zinthu zina, sangalalani ndi zimene mumakwanitsa kucita. Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anali mkaidi kwa zaka zambili, ndipo sanathe kupitiliza umishonale. Koma nthawi iliyonse imene anthu ena anali kupita kukamucezela, iye anali kulankhula nao za m’Malemba ndi kuwalimbikitsa mwakuuzimu.—Mac. 28:16, 30, 31.

15. N’cifukwa ciani Akristu acikulile timawayamikila kwambili?

15 Yehova amayamikilanso zimene acikulile amacita muutumiki wake. Ngakhale kuti Solomo anakamba kuti ukalamba ndi nthawi yovuta, Yehova amayamikila zonse zimene Akristu acikulile amacita pom’tumikila. (Luka 21:2-4) Abale ndi alongo amayamikila citsanzo cabwino ca kukhulupilika ndi kupilila cimene abale ndi alongo acikulile amasonyeza.

16. Kodi Anna analibe mwai wotani? Nanga anacita ciani kuti atumikile Mulungu?

16 Baibo imachula za mkazi wina dzina lake Anna amene sanasiye kutamanda Yehova mu ukalamba wake. Pamene Yesu anali kubadwa, mkazi wamasiye ameneyu anali ndi zaka 84. N’zoonekelatu kuti mkazi ameneyu anafa asanakhale wophunzila wa Yesu ndiponso asanadzozedwe ndi mzimu woyela kapena asanayambe kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Koma Anna anasangalala kucita zimene akanatha. Iye “sanali kusoŵa pakacisi. Anali kucita utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Luka 2:36, 37) Pamene wansembe anali kufukiza nsembe usana ndi usiku m’kacisi, Anna anali kukhala pakati pa khamu la anthu amene anali kusonkhana m’bwalo la kacisi. Panthawiyo iye anali kupemphela ca mumtima mwina kwa mphindi 30. Pamene anaona Yesu ali wakhanda, iye “analankhula za mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezela cipulumutso ca Yerusalemu.”—Luka 2:38.

17. Kodi tingathandize bwanji Akristu okalamba ndi odwala kuti azitengako mbali pakulambila koona?

17 Masiku ano, tiyenela kupeza mipata ya mmene tingathandizile Akristu okalamba kapena odwala. Ena amafunitsitsa kufika pa misonkhano ya mpingo kapena ikulu-ikulu, koma thanzi lao limawalepheletsa kutelo. M’maiko ena, mipingo imapanga makonzedwe akuti okalamba ndi odwala azimvetsela misonkhano pafoni. Koma zimenezo n’zosatheka ku maiko ena. Ngakhale zili conco, Akristu amene sangathe kupezeka pamisonkhano akhoza kucilikiza kulambila koona. Mwacitsanzo, mapemphelo ao angathandize kuti mpingo ulimbe mwa kuuzimu.—Ŵelengani Salimo 92:13, 14.

18, 19. (a) N’cifukwa ninji nthawi zina Akristu okalamba sangadziŵe mmene citsanzo cao cimalimbikitsila ena? (b) Ndani amene ayenela kugwilitsila nchito uphungu wakuti: “Kumbukila Mlengi wako Wamkulu”?

18 Akristu okalamba sangadziŵe mmene citsanzo cao cimalimbikitsila ena. Mwacitsanzo, ngakhale kuti Anna anali kutumikila mokhulupilika pa kacisi, mwina iye sanadziŵe kuti citsanzo cake cidzalimbikitsa ena mtsogolo. Citsanzo ca Anna cokonda Yehova cinalembedwa m’Baibo. Mofananamo, abale ndi alongo anu sadzaiŵala cikondi cimene muli naco pa Mulungu. Ndiye cifukwa cake Mau a Mulungu amati: “Imvi ndizo cisoti cacifumu ca ulemelelo zikapezeka m’njila yacilungamo.”—Miy. 16:31.

19 Aliyense wa ife ayenela kudziŵa kuti sangakwanitse kucita zonse potumikila Yehova. Koma ena a ife amene tikaliko ndi mphamvu, tizikumbukila mau ouzilidwa akuti: “Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako, asanafike masiku oipa.”—Mlal. 12:1.