NKHANI YA PACIKUTO | BOMA LOPANDA ZIPHUPHU
Ufumu wa Mulungu Ndi Boma Lopanda Ziphuphu
Pofotokoza maganizo ake pankhani ya ziphuphu za m’boma, mkulu wa dipatimenti ya boma yoona za kayendetsedwe ka ndalama m’dziko la Nicaragua anakamba kuti: “Ngati nzika za dziko ndi za ziphuphu, akuluakulu a boma sangalephele kukhala a ziphuphu cifukwa naonso ndi anthu.”
Kodi si zoona kuti ngati anthu m’dziko ndi a ziphuphu, boma limene angapange nalonso limakhala la ziphuphu? Ngati n’conco ndiye kuti boma locokela kwinakwake osati lopangidwa ndi anthu ndi limene lingakhale lopanda ziphuphu. Baibulo limafotokoza za boma lotelo. Boma limenelo ndi Ufumu wa Mulungu umene Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuti azipempha kuti ubwele.—Mateyu 6:9, 10.
Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni limene likulamulila kucokela kumwamba. Bomali lidzaloŵa m’malo mwa maboma onse a anthu. (Salimo 2:8, 9; Chivumbulutso 16:14; 19:19-21) Cimodzi mwa zinthu zimene Ufumu wa Mulungu udzacita n’cakuti udzathetsa maboma onse a anthu cifukwa amacita ziphuphu. Onani zinthu 6 zimene zimatsimikizila kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa ziphuphu.
1. MPHAMVU ZAKE
VUTO: Nthawi zambili maboma a anthu amapeza ndalama zoyendetsela boma mwa kulamula nzika zao kupeleka misonkho. Njila imeneyi yopezela ndalama imapangitsa kuti akuluakulu ena a boma aziba ndalama. Enanso amalandila ziphuphu kwa anthu amene amafuna kupeleka ndalama zocepa za msonkho kapena ndalama zina zimene amafunika kulipila ku boma. Vuto limeneli limapangitsanso kuti boma likweze misonkho kuti lipeze ndalama zimene zataika cifukwa ca ziphuphu. Boma likakweza misonkho, anthu amacitanso ziphuphu kwambili. Zinthu zikakhala telo, anthu oona mtima ndi amene amavutika kwambili.
NJILA YOTHETSELA VUTOLI: Mphamvu zoyendetsela Ufumu wa Mulungu ndi zocokela kwa Yehova Mulungu. * (Chivumbulutso 11:15) Ufumuwu sulandila misonkho kucokela kwa nzika zake kuti lipeze ndalama zoyendetsela boma lake. Koma popeza kuti Mulungu ali ndi ‘mphamvu zoopsa,’ n’zosacita kufunsa kuti Ufumuwu udzapatsa nzika zake zinthu zoculuka zofunikila.—Yesaya 40:26; Salimo 145:16.
2. WOLAMULILA WAKE
VUTO: Amai Susan Rose-Ackerman, amene tawachula m’nkhani yapita anakamba kuti nchito yothetsa ziphuphu “ifunika kuyambila kwa akuluakulu a boma.” Anthu amaleka kukhulupilila boma limene limayesa kuthetsa cabe ziphuphu za apolisi ndi oyang’anila za oloŵa ndi otuluka m’dziko, koma amalekelela akuluakulu a boma amenenso amacita ziphuphu. Komanso ngakhale wolamulila wakhalidwe labwino kwambili amakhala wosadalilika kwenikweni cifukwa ndi wopanda ungwilo. Conco, Baibulo limanena kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amacita zabwino zokhazokha.”—Mlaliki 7:20.
Yesu anakana ciphuphu cacikulu koposa
NJILA YOTHETSELA VUTOLI: Mulungu anasankha Yesu Kristu kukhala Wolamulila wa Ufumu wake. Mosiyana ndi anthu opanda ungwilo, Yesu sangakopeke ndi zoipa. Iye anasonyeza kuti sangakopeke ndi zoipa pamene anakana ciphuphu cacikulu koposa cakuti apatsidwe “maufumu onse a padziko ndi ulemelelo wao.” Mdyelekezi analonjeza Yesu kuti adzamupatsa maufumu a dziko ndi ulemelelo wao ngati atamugwadila, koma iye anakana. (Mateyu 4:8-10; Yohane 14:30) Ngakhale pamene anali kuzunzidwa mpaka kuphedwa, Yesu anatsimikiza mtima kukhalabe wokhulupilika. Iye anakana cakumwa caukali cimene cikanamucepetsela ululu koma cikanapangitsa kuti asacite zinthu mwanzelu. (Mateyu 27:34) Yesu anaukitsidwa ndi Mulungu ndipo tsopano ali ndi moyo kumwamba. Cifukwa ca zimenezi, iye waonetsa kuti ndi Mfumu yabwino kwambili ya Ufumu wa Mulungu.—Afilipi 2:8-11.
3. KUDALILIKA KWAKE
VUTO: M’maiko ambili mumacitika masankho nthawi ndi nthawi. Anthu amaganiza kuti kucita zimenezi kumawapatsa mwai wocotsa paudindo olamulila osakhulupilika. Koma zoona zake n’zakuti nthawi zambili pa makampeni ndi pa masankho pamacitika zacinyengo, ngakhale m’maiko olemela. Mwa kupatsa anthu zinthu pa kampeni kapena kucita zinthu zina zake, olemela anganyengelele anthu kuti asankhe munthu amene io akufuna.
Woweluza wina wa khoti lalikulu ku United States, dzina lake John Paul Stevens analemba kuti cifukwa ca cinyengo cimene cimacitika pa masankho, “Boma limakhala lopanda cilungamo ndipo anthu amalikaikila.” Motelo n’zosadabwitsa kuti anthu ambili amaganiza kuti andale ndi amene amacita ziphuphu kwambili kuposa anthu onse.
NJILA YOTHETSELA VUTOLI: Mu Ufumu wa Mulungu simudzakhala kampeni kapena masankho cifukwa cakuti ufumuwu udzalamulila kosatha. (Danieli 7:13, 14) Popeza kuti Mulungu ndiye anasankha Wolamulila wa Ufumu wake, anthu sacita masankho ndiponso sangauthetse. Zinthu zabwino zimene Ufumuwu umacitila nzika zake n’zokhalitsa cifukwa cakuti ulamulilo wake ndi wosatha.
4. MALAMULO AKE
VUTO: Mwina mungaganize kuti kuika malamulo atsopano kungathandize kuthetsa ziphuphu. Koma akatswili apeza kuti nthawi zambili kuculukitsa malamulo kumangopangitsa kuti anthu azicita ziphuphu kwambili. Kuonjezela pamenepo, kaŵilikaŵili boma limaononga ndalama zambili pofuna kuonetsetsa kuti anthu akutsatila malamulo oletsa ziphuphu, koma zimenezi sizithandiza kwenikweni.
NJILA YOTHETSELA VUTOLI: Malamulo a Ufumu wa Mulungu ndi apamwamba kwambili kuposa malamulo a maboma a anthu. Mwacitsanzo, m’malo mopeleka mndandanda wa malamulo ambilimbili, Yesu anapeleka lamulo limene limachedwa Khalidwe Lopambana. Iye anati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.” (Mateyu 7:12) Cocititsa cidwi kwambili n’cakuti malamulo a Ufumu wa Mulungu amaongolela maganizo ndi zocita za anthu. Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mateyu 22:39) Ndipo Mulungu angathe kudziŵa kuti munthu ali ndi maganizo abwino kapena ai cifukwa iye amaona za mumtima.—1 Samueli 16:7.
5. ZOLINGA ZAKE
VUTO: Dyela ndi kudzikonda n’zimene zimacititsa kuti anthu azicita ziphuphu. Akuluakulu a boma ndiponso anthu a m’dziko nthawi zambili amacita zinthu mwadyela ndi modzikonda. Mwacitsanzo, sitolo yaikulu ya ku Seoul imene tachula m’nkhani yapita ija inagwa cifukwa cakuti akuluakulu a boma analola omanga sitoloyo kugwilitsila nchito zipangizo zosalimba ndi kuphwanya malamulo a kamangidwe kovomelezeka. Akuluakulu a boma analandila ciphuphu ku kampani ya zomangamanga kuti asaononge ndalama zambili pomanga sitoloyo.
Kuti ziphuphu zithe, anthu afunika kuphunzitsidwa kuti adziŵe mmene angathetsele mtima wa dyela ndi wodzikonda. Komabe, maboma a anthu amalephela kuphunzitsa anthu makhalidwe abwino ndipo sangakwanitse kutelo.
NJILA YOTHETSELA VUTOLI: Ufumu wa Mulungu ukuthetsa ziphuphu mwa kuphunzitsa anthu mmene angacotsele maganizo oipa amene amayambitsa ziphuphu. * Maphunzilo amenewa amathandiza anthuwo ‘kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo ao.’ (Aefeso 4:23) Iwo aphunzila ‘kukhala okhutila ndi zimene ali nazo’ ndi kukhala ‘oganizila zofuna za ena’ m’malo mwa kukhala adyela ndi odzikonda.—Afilipi 2:4; 1 Timoteyo 6:6.
6. NZIKA ZAKE
VUTO: Ngakhale zinthu m’dziko zitakhala kuti zikuyenda bwino ndiponso anthu akulandila maphunzilo abwino kwambili, ena angasankhe kucita zinthu mosakhulupilika. Akatswili amakamba kuti ndiye cifukwa cake maboma sangakwanitse kuthetsa ziphuphu. Mabomawo amacepetsako cabe ziphuphu ndi zotsatila zake zoipa.
NJILA YOTHETSELA VUTOLI: Bungwe lina lolimbana ndi ziphuphu linanena kuti maboma afunika kuphunzitsa anthu kukhala “okhulupilika, oona mtima, ndi odalilika” kuti akwanitse kuthetsa ziphuphu. Kucita zimenezi n’kofunika, ndipo Ufumu wa Mulungu umalimbikitsa nzika zake kukhala ndi makhalidwe amenewa. Kuposa pamenepo, Ufumu wa Mulungu umalamula nzika zake kukhala ndi makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, Baibulo limanena kuti “aumbombo” ndi “abodza” sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.—1 Akorinto 6:9-11; Chivumbulutso 21:8.
N’zotheka anthu kuphunzila ndi kutsatila mfundo za makhalidwe abwino zimenezi monga mmene anacitila Akristu a m’nthawi ya atumwi. Mwacitsanzo, pamene wophunzila wina dzina lake Simoni anapempha kuti agule mzimu woyela kwa atumwi, io anakana kulandila ciphuphu ndipo anamuuza kuti: “Lapa coipa cakoci.” Pamene Simoni anadziŵa kuti maganizo ake anali olakwika, anapempha atumwiwo kuti amupemphelele kuti athetse maganizo akewo.—Machitidwe 8:18-24.
ZIMENE MUNGACITE KUTI MUKHALE NZIKA YA UFUMU WA MULUNGU
Kaya mumakhala m’dziko liti, muli ndi mwai wokhala nzika ya Ufumu wa Mulungu. (Machitidwe 10:34, 35) Maphunzilo amene Ufumu wa Mulungu ukupeleka kwa anthu padziko lonse lapansi angakuthandizeni kudziŵa zimene mungacite kuti mukhale nzika ya Ufumuwu. Mboni za Yehova zingakonde kukuonetsani mmene zimaphunzilila Baibulo ndi anthu kwaulele, ndipo phunziloli limakhala la mphindi 10 kapena kuposelapo mlungu uliwonse. Zinthu zina zimene mungaphunzile pa phunziloli ndi zokhudza “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu,” ndi mmene udzathetsela ziphuphu za m’boma. (Luka 4:43) Tikupemphani kuti mukambilane ndi Mboni za Yehova m’dela lanu kapena pitani pa Webusaiti yathu ya jw.org.