Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Munakhumudwa ndi Mulungu?

Kodi Munakhumudwa ndi Mulungu?

“N’CIFUKWA ciani zimenezi zandicitikila? N’cifukwa ciani Mulungu walola kuti zimenezi zindicitikile?” Mafunso amenewa ndi amene Sidnei wazaka 24, wa ku Brazil amadzifunsa. Iye anacita ngozi m’mbali mwa mtsinje ndipo analemala n’kumayendela pa kanjinga ka olemala.

Mavuto amene amabwela cifukwa ca ngozi, kudwala, imfa ya munthu amene timakonda, ngozi za cilengedwe kapena nkhondo, zingacititse anthu kukhumudwa ndi Mulungu mosavuta. Zimenezi sizacilendo. Mwamuna wam’nthawi zakale Yobu, anakumana ndi mavuto motsatizanatsatizana. Mwamunayu anaimba Mulungu mlandu mwa kunena kuti: “Ndimafuulila kwa inu kuti mundithandize, koma simundiyankha. Conco ndaimilila kuti mundimvele. Mwasintha n’kukhala wankhanza kwa ine. Ndi mphamvu yonse ya dzanja lanu, mwandisungila cidani.”—Yobu 30:20, 21.

Yobu sanadziŵe kumene mavuto ake anali kucokela, cifukwa cake mavuto anamugwela kapena cimene Mulungu analolela kuti mavutowo amucitikile. Koma cokondweletsa n’cakuti, Baibulo limatiuza cifukwa cake zinthu zotelezi zimaticitikila ndi mmene tiyenela kucitila tikakumana ndi mavuto.

KODI MULUNGU ANAFUNA KUTI ANTHU AZIVUTIKA?

Ponena za Mulungu, Baibulo limati: “Nchito yake ndi yangwilo, Njila zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupilika, amene sacita cosalungama. Iye ndi wolungama ndi woongoka.” (Deuteronomo 32:4) Ngati n’conco, kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu amene ndi “wolungama ndi woongoka” acititse mavuto n’colinga cakuti alange anthu kapena kuwayeletsa?

Ai ndithu, Baibulo limatiuza kuti: “Munthu akakhala pa mayeselo asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Baibulo limatiphunzitsa kuti Mulungu anapanga anthu angwilo. Iye anapatsa Adamu ndi Hava, malo okongola okhalamo, zonse zofunika paumoyo, ndi nchito yabwino ndi yokhutilitsa. Mulungu anawauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi.” Kunena zoona, Adamu ndi Hava analibe cifukwa cokhumudwila ndi Mulungu.—Genesis 1:28.

Koma masiku ano, zinthu ndi zosiyana ndi mmene zinalili anthu ali angwilo. M’mbili yonse ya anthu mavuto akukulilakulilabe. Ndipo mau otsatilawa akukwanilitsidwa. Mauwo amati: “Cilengedwe conse cikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) N’ciani cinacitika?

N’CIFUKWA CIANI TIMAVUTIKA?

Kuti timvetse cifukwa cake timavutika, tifunika kukumbukila zimene zinacitika poyamba. Mosonkhezeledwa ndi mngelo wopanduka, amene anadzachedwa kuti Satana Mdyelekezi, Adamu ndi Hava, anakana kutsatila malamulo a Mulungu osiyanitsa cabwino ndi coipa mwa kudya “zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa.” Mdyelekezi anauza Hava kuti ngakhale ataphwanya malamulo a Mulungu, sadzafa, ndipo ananena kuti Mulungu ndi wabodza. Satana ananenanso kuti Mulungu amamana anthu ufulu wosankha okha cabwino ndi coipa. (Genesis 2:17; 3:1-6) M’mau ena, Satana anakamba kuti anthu akhoza kudzilamulila bwino popanda Mulungu. Zonsezi zinayambitsa nkhani yofunika kwambili yakuti, kodi Mulungu ndi woyenelela kulamulila anthu?

Mdyelekezi anayambitsanso nkhani ina yofunika kwambili. Iye anakaikila ngati anthu amatumikila Mulungu ndi mtima wonse. Ponena za munthu wokhulupilika Yobu, Mdyelekezi anauza Mulungu kuti: “Kodi inuyo simwam’chinga iyeyo? Mwachingilanso nyumba yake ndi ciliconse cimene ali naco . . . Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!” (Yobu 1:10, 11) Ngakhale kuti mau a Satana anali kukhudza Yobu cabe, iye anatanthauzanso kuti anthu onse amatumikila Mulungu ndi mtima wadyela.

MMENE MULUNGU ANATHETSELA NKHANIZO

Kodi Mulungu akanacita ciani kuti athetse nkhani zimenezo? Mulungu, amene ndi wanzelu zozama, anapeza njila yabwino kwambili yothetsela nkhanizo, iye sanatisiye cabe kuti tikhumudwe. (Aroma 11:33) Iye analola anthu kuyamba kudzilamulila okha kwa kanthawi, n’colinga cakuti aonetse kuti ndani ali woyenela kulamulila anthu.

Mavuto onse ali padziko lapansi, ndi umboni wakuti anthu alephelelatu kudzilamulila okha. Maboma a anthu alephelanso kubweletsa mtendele, citetezo, ndi cisangalalo ndipo aononga ngakhale dziko lapansi. Zocitika zonsezi zikukwanilitsa mfundo yofunika kwambili ya m’Baibulo yakuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo woongolela mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ulamulilo wa Mulungu wokha ndi umene udzabweletsa mtendele weniweni ndi cisangalalo. Ndiponso padziko lapansi sipadzapezeka munthu wosauka, cifukwa ndico colinga ca Mulungu.—Yesaya 45:18.

Kodi Mulungu adzakwanilitsa bwanji colinga cake kwa anthu? Kumbukilani kuti Yesu anauza ophunzila ake kupemphela kuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Zoonadi, panthawi yake yoikika, Mulungu, kudzela mu Ufumu wake, adzacotsa mavuto onse padziko lapansi. (Danieli 2:44) Umphawi, matenda, ndi imfa sizidzakhalakonso. Ponena za wosauka, Baibulo limatiuza kuti Mulungu “adzalanditsa wosauka wofuulila thandizo.” (Salimo 72:12-14) Baibulo limalonjezanso kuti: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Ponena za okondedwa athu amene anamwalila amene Mulungu akuwakumbukila, Yesu anakamba kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda acikumbutso adzamva mau ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Malonjezo amenewa ndi osangalatsa kwambili.

Kulimbitsa cikhulupililo cathu m’malonjezo a Mulungu kudzatithandiza kuti tisakhumudwe ndi Mulungu tikakumana ndi mavuto

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUSAKHUMUDWE

Patapita zaka 17, pambuyo pa ngozi imene inacitikila Sidnei, amene tamuchula kuciyambi kwa nkhani ino, iye anakamba kuti: “Sindinaimbe Yehova Mulungu mlandu cifukwa ca ngozi imene inandicitikila, koma n’zoona kuti poyamba ndinakhumudwa ndi iye. Nthawi zina ndikaganizila za thanzi langa tsopano, ndimakhumudwa ndipo ndimalila. Komabe, Baibulo landithandiza kudziŵa kuti ngozi imeneyo siinali cilango cocokela kwa Mulungu. Baibulo limati, ‘nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimatigwela tonsefe.’ Kupemphela kwa Yehova ndi kuŵelenga Baibulo kwandithandiza kukhala ndi maganizo oyenela.”—Mlaliki 9:11; Salimo 145:18; 2 Akorinto 4:8, 9, 16.

Kudziŵa zifukwa zimene Mulungu walolela mavuto kuticitikila, ndi kuti posacedwapa iye adzacotsa mavuto amenewa, kudzatithandiza kusakhumudwa ndi Mulungu tikakumana ndi mavuto alionse. Mulungu amatitsimikizila kuti “amapeleka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Palibe wokhulupilila iye, ndi Mwana wake amene adzakhumudwe.—Aheberi 11:6; Aroma 10:11.