N’cifukwa Ciani Anthu Amapemphela?
“Ndinali kukonda kuchova njuga kwambili. Conco ndinapemphela kuti ndipambane. Koma pemphelo langa silinayankhidwe.”—Samuel, * wa ku Kenya.
“Kusukulu, tonse tinali kufunika kupeleka pemphelo loloweza pamtima limene tinaphunzitsidwa.”—Teresa, wa ku Philippines.
Ndikakumana ndi mavuto ndimapemphela. Ndimapempha Mulungu kuti andikhululukile ndi kundithandiza kukhala Mkristu wabwino.”—Magdalene, wa ku Ghana.
Zimene Samuel, Teresa, ndi Magdalene anakamba zikuonetsa kuti anthu amapemphela pa zifukwa zosiyanasiyana, ndipo zifukwa zina ndi zomveka koma zina sizomveka. Mapemphelo a anthu ena amacokela pansi pa mtima koma a ena sacokela pansi pa mtima. Motelo, kaya munthu apemphele n’colinga cakuti acite bwino mayeso kusukulu, kupambana pa maseŵela ena ake, kuti Mulungu atsogolele banja lake kapena pa zifukwa zina, anthu mamiliyoni ambili amaona kuti kupemphela n’kofunika. Kafukufuku wina anaonetsa kuti ngakhale anthu amene sapita ku chalichi, amapemphela nthawi zonse.
Kodi inu mumapemphela? Ngati ndi conco, mumapemphela pa zinthu ziti? Kaya mumakonda kupemphela kapena ai, mungadzifunse kuti: ‘Kodi kupemphela kuli ndi ubwino wanji? Kodi pali winawake amene akundimvetsela?’ Wolemba wina anakamba kuti pemphelo lili ngati “mankhwala . . . amene amathandiza kuti munthu amveleko bwino.” Madokotala ena amaonanso kuti pemphelo ndi “njila ina yocilitsila.” Kodi pemphelo liyenela kukhala cizolowezi cabe kapena kukhala ngati mankhwala amene angatithandize kumvelako bwino tikadwala?
Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limakamba kuti pemphelo limaposa mankhwala. Limatiuza kuti winawake amamvetsela mapemphelo amene amapelekedwa m’njila yoyenela, ndi opempha zinthu zoyenela. Kodi zimenezi n’zoona? Tiyeni tione umboni wake.
^ par. 2 Maina ena asinthidwa.