Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
Kodi akufa adzakhalanso ndi moyo?
Yehova Mulungu ndiye Kasupe wa moyo. (Salimo 36:9) Ndiye cifukwa cake m’pomveka kuti iye adzaukitsa akufa. Baibulo limatitsimikizila kuti Mulungu adzacitadi zimenezi mtsogolo. (Ŵelengani Machitidwe 24:15) Nanga n’cifukwa ciani adzaukitsa akufa?
Colinga ca Mlengi wathu poyamba cinali cakuti anthu akhale ndi moyo wosatha padziko lapansi. (Genesis 1:31; 2:15-17) Colinga cake cimeneci sicinasinthe. Iye zimam’pweteka kwambili akaona kuti anthufe tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana, komanso kuti tili ndi moyo waufupi.—Ŵelengani Yobu 14:1, 14, 15.
Kodi amene adzaukitsidwa adzakhala kuti?
Kodi Mulungu analenga anthu kuti azikhala kumwamba? Iyai. Mulungu analenga angelo kuti azikhala kumwamba. Koma anthu anawalenga kuti azikhala padziko lapansi. (Genesis 1:28; Yobu 38:4, 7) Mwacitsanzo, ganizilani anthu amene Yesu anaukitsa. Iwo ataukitsidwa, anakhalanso ndi moyo padziko lapansi. Conco, anthu ambili amene adzaukitsidwa adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi.—Ŵelengani Yohane 5:28, 29; 11:44.
Komabe, Mulungu anasankha anthu ocepa kuti adzakhale kumwamba ndipo adzapatsidwa matupi auzimu. (Luka 12:32; 1 Akorinto 15:49, 50) Anthu amene adzaukitsidwila kumwamba adzalamulila dziko lapansi limodzi ndi Yesu.—Ŵelengani Chivumbulutso 5:9, 10.