Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Buku Losavuta Kumvetsetsa

Buku Losavuta Kumvetsetsa

Baibulo ndi buku lakale kwambili. Kodi lakhalapo kwa zaka zingati? Baibulo linayamba kulembedwa ku Middle East zaka 3,500 zapitazo. Nthawiyo, mpamene ulamulilo wotsatizana wa m’banja la mafumu a Cichainizi ochulidwa m’mbili yakale unayamba, komanso kutatsala zaka 1000 kuti cipembedzo ca Cibuda ciyambe m’dziko la India.—Onani bokosi lakuti “Dziŵani Izi Ponena za Baibulo.”

Baibulo limapeleka mayankho ogwila mtima a mafunso ofunika kwambili

Kuti buku likhale lothandiza ndiponso lofunika kwambili kwa anthu, liyenela kukhala losavuta kumvetsetsa. Umu ndi mmene Baibulo lilili. Limapeleka mayankho ogwila mtima a mafunso ofunika kwambili.

Mwacitsanzo, kodi munadzifunsapo kuti, ‘N’cifukwa ciani tili ndi moyo?’ Funso limeneli lagometsa mutu anthu kwa zaka masauzande ambili. Komabe, yankho la funso limeneli lipezeka m’macaputala aŵili oyambilila a Genesis, buku loyamba m’Baibulo. M’macaputala amenewa, Baibulo limatiuza za “ciyambi,” pamene zinthu monga milalang’amba, nyenyezi, ndi dziko lapansi zinalengedwa zaka mabiliyoni ambili zapitazo. (Genesis 1:1) Limatiuzanso mmene dziko lapansi linalengedwela kuti pakhale zamoyo, mmene zamoyo zosiyanasiyana zinakhalilapo, ndiponso kulengedwa kwa anthu. Baibulo limatiuza colinga cimene Mulungu analengela zinthu zonsezi.

N’LOSAVUTA KUMVETSETSA

Baibulo lili ndi malangizo amene amatithandiza kulimbana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku. Malangizo amenewo si ovuta kumvetsetsa. Onani mbali ziŵili izi.

Mbali yoyamba, mau a m’Baibulo ndi osavuta, acindunji, ndiponso osangalatsa. M’malo moseŵenzetsa mau ambili ovuta kumvetsetsa, Baibulo lili ndi mau amene timawadziŵa bwino. Mbali zovuta anazilemba m’mau amene timakamba tsiku lililonse.

Mwacitsanzo, Yesu anafotokoza mafanizo ambili osavuta okamba za zinthu zimene anthu anali kudziŵa bwino. Anacita zimenezo n’colinga cakuti awafike pamtima. Ambili mwa mafanizo amenewo anawachula mu ulaliki wake wa pa phili, wolembedwa m’buku la m’Baibulo la Mateyu macaputala 5 mpaka 7. Katswili wina wa Baibulo anacha ulalikiwu kuti “nkhani yothandiza,” ndipo anakamba kuti colinga ca ulalikiwo ndi “kutitsogolela paumoyo wathu, osati kutidziŵitsa zinthu zosiyanasiyana. Mungaŵelenge macaputala amenewo mwina kwa mphindi 15 kapena 20, ndipo mudzadabwa ndi mau a Yesu osavuta koma amphamvu kwambili.

Mbali yaciŵili imene imacititsa Baibulo kukhala losavuta kumvetsetsa ndi nkhani zake. Baibulo si buku la nthano. Buku lakuti The World Book Encyclopedia linakamba kuti Baibulo ndi buku limene “limakamba za anthu apamwamba ndi otsika,” komanso “zolinga zao, zolakwa zao, ndi zipambano zao.” Si covuta kumvetsetsa ndi kufotokoza nkhani za anthu enieni amenewo, ndiponso zimene timaphunzila kwa io.—Aroma 15:4.

LIKUPEZEKA M’ZINENELO ZAMBILI

Kuti mumvetsetse zimene mukuŵelenga m’buku, ilo liyenela kukhala la cinenelo cimene mudziŵa. Mwacionekele, Baibulo nalonso likupezeka m’cinenelo cimene mumamvetsetsa, mosasamala kanthu za kumene mumakhala kapena mtundu wanu. Onani nchito imene imakhalapo kuti Baibulo lizipezeka m’zinenelo zambili.

Nchito Yomasulila. Poyamba, Baibulo linalembedwa m’Ciheberi, m’Ciaramu, ndi m’Cigiriki. Izi zinacititsa kuti liziŵelengedwa ndi anthu ocepa. Pofuna kuti Baibulo lipezeke m’zinenelo zinanso, omasulila mabuku akhala akugwila nchito mwakhama. Cifukwa ca khama lao, Baibulo likupezeka m’zinenelo pafupifupi 2,700 kaya lathunthu kapena mbali yake. Izi zitanthauza kuti anthu oposa 90 pa anthu 100 alionse ali ndi Baibulo m’cinenelo cao.

Nchito Yofalitsa Mabuku. Poyamba, Baibulo linalembedwa pazinthu zosacedwa kuonongeka, monga pamipukutu yamapepala a gumbwa ndi zikopa. Kuti uthengawo ufalikile, anali kukopela zolembedwazo bwinobwino ndi manja. Makope amenewo anali okwela mtengo, ndipo ndi anthu ocepa amene anali kupezeka nao. Komabe, pogwilitsila nchito makina osindikizila amene Gutenberg anapanga zaka zoposa 550 zapitazo, Baibulo linayamba kufalitsidwa kwambili. Mabaibulo oposa 5 biliyoni afalitsidwa, kaya athunthu kapena mbali yake.

Palibe buku lina lacipembedzo limene limafanana ndi Baibulo pa mfundo zimene tafotokozazi. Kukamba zoona, Baibulo ndi buku losavuta kumvetsa. Komabe, ena zimawavuta kulimvetsetsa. Ngakhale n’conco, thandizo lilipo. Kodi mungalipeze kuti? Nanga mungapindule bwanji? Ŵelengani nkhani yotsatila kuti mudziŵe mayankho a mafunso amenewa.