Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Kodi zidzatheka kuti padziko lapansi pakhale cilungamo ceni-ceni?
Kodi mungayankhe bwanji?
Inde
Iyai
Kapena
Zimene Baibo imakamba
“Ndikudziŵa bwino kwambili kuti Yehova adzazengela mlandu anthu osautsika. Iye adzacitila cilungamo anthu osauka.” (Salimo 140:12) Ufumu wa Mulungu udzabweletsadi cilungamo ceni-ceni padziko lapansi.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Mulungu amaona zinthu zopanda cilungamo zimene zikucitika, ndipo adzazithetsa.—Mlaliki 5:8.
Cilungamo ca Mulungu cidzabweletsa mtendele na citetezo padziko lapansi.—Yesaya 32:16-18.
Kodi Mulungu amakondela?
Ena amakhulupilila kuti Mulungu amadalitsa na kutembelela anthu ena. Ena amakhulupilila kuti Mulungu amaona anthu onse cimodzi-modzi. Nanga imwe muganiza bwanji?
Zimene Baibo imakamba
“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Mulungu amaona anthu onse cimodzi-modzi.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Baibo ili na “uthenga wabwino” wopita “kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.”—Chivumbulutso 14:6.