Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

kovop58/stock.adobe.com

KHALANI MASO!

Kodi Masewela a ma Olympic Angagwilizanitsedi Anthu?—Kodi Baibulo Ikutipo Ciyani?

Kodi Masewela a ma Olympic Angagwilizanitsedi Anthu?—Kodi Baibulo Ikutipo Ciyani?

 Mu caka ca 2024, anthu pafupifupi 5 biliyoni akhala akupenyelela masewela a ma Olympic a pakati pa maiko okwana 206. Thomas Bach, amene ni mtsogoleli wa bungwe la International Olympic Committee, anati: “Zimene tikucitazi zidzagwilizanitsa anthu padziko lonse ndi kubweletsa mtendele. Tiyeni ticite zimene masewelawa akulimbikitsa kuti anthu onse azikhala mwamtendele komanso mogwilizana, ngakhale kuti ndife osiyana.”

 Kodi masewela a ma Olympic angakwanitsedi kucita zimenezi? Kodi n’zotheka anthu kudzakhala ndi mtendele weniweni komanso mgwilizano?

Kodi masewelawa angabweletsedi mtendele ndi mgwilizano?

 Ma Olympic a caka cino apangitsa anthu kuganizila zinthu zambili zosiyanasiyana, osati masewela okha. Masewelawa akulimbikitsa zandale komanso nkhani zina zimene zikugawanitsa anthu. Izi ziphatikizapo nkhani zokhudza maufulu a anthu, kusankhana mitundu, kusalana cifukwa cosiyana zipembedzo, komanso kusankhana pa nkhani zacuma.

 Masewela a maiko onse, monga ma Olympic, amasangalatsa anthu. Koma pa zocitika zimenezi anthu amacita zinthu zimene zimabweletsa magawano. Ndipo zocitikazi zimalimbikitsa anthu kupitiliza kucita zinthu zimenezi, m’malo mocita zinthu zomwe zingabweletse mtendele weniweni komanso mgwilizano.

 Baibulo linakambilatu kuti anthu adzakhala ndi makhalidwe amene adzacititsa kuti cikhale covuta kubweletsa mgwilizano padziko. (2 Timoteyo 3:1-5) Kuti mudziwe zambili za ulosi wa m’Baibulo umenewu, welengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?

Ciyembekezo ceniceni ca mtendele ndi mgwilizano wa padziko lonse

 Baibulo limapeleka ciyembekezo ceniceni ca mtendele ndi mgwilizano wa padziko lonse. Limalonjeza kuti anthu onse padziko lapansi adzakhala ogwilizana mu ulamulilo wa boma lakumwamba lochedwa “Ufumu wa Mulungu.”—Luka 4:43; Mateyo 6:10.

 Mfumu ya Ufumu umenewo, amene ndi Yesu Khristu, adzabweletsa mtendele padziko lonse. Baibulo limati:

  •   “Wolungama zinthu zidzamuyendela bwino, ndipo padzakhala mtendele woculuka.”—Salimo 72:7.

  •   “Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo. . . Adzawapulumutsa kuti asapondelezedwe komanso kucitilidwa zaciwawa.”—Salimo 72:12, 14.

 Ngakhale masiku ano, zimene Yesu anaphunzitsa zagwilizanitsa anthu mamiliyoni m’maiko 239. Monga Akhristu, Mboni za Yehova padziko lonse zaphunzila kukhala anthu amtendele. Kuti mumve zambili, welengani magazini ya Nsanja ya Mlonda ya mutu wakuti “N’zotheka Kugonjetsa Cidani.