Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Left: Yasser Qudaih/Anadolu via Getty Images; right: RONALDO SCHEMIDT/AFP via Getty Images

KHALANI MASO!

Kodi Nkhondo Zidzatha Liti?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Kodi Nkhondo Zidzatha Liti?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 “Ino ndiyo nthawi yofunika kupewa kucita zinthu zimene zingakulitse mkangano. Ndiyo nthawi yofunika kudziletsa kwambili,” anatelo António Guterres, Kalembela Wamkulu wa Bungwe la United Nations pothilila ndemanga pa zimene dziko la Iran linacita zoponya mizinga m’dziko la Israel pa Ciŵelu, pa April 13, 2024.

 Nkhondo imene ikucitika ku Middle East n’citsanzo cimodzi cabe ca zimene zikucitika padziko lonse.

 “Kucokela pamene nkhondo yaciŵili ya padziko lonse inatha nkhondo zakhala zikucitika padziko lapansi, koma pa nthawi ino zaculuka kwambili ndipo zikukhudza anthu 2 biliyoni. Izi zionetsa kuti munthu mmodzi pa anthu anayi alionse akukhudzidwa.”—Linatelo lipoti la United Nations Security Council, pa January 26, 2023.

 Maiko amene muli nkhondo ni Israel, Gaza, Syria, Azerbaijan, Ukraine, Sudan, Ethiopia, Niger, Myanmar, komanso, Haiti. a

 Kodi nkhondozi zidzatha liti? Kodi olamulila a dzikoli angabweletse mtendele? Kodi Baibo ikutipo ciyani?

Dziko lili pa nkhondo

 Nkhondo zimene zikucitika padziko lonse masiku ano, ni umboni wakuti posacedwapa nkhondo zonse zidzathelatu. Nkhondozi zikukwanilitsa ulosi wa m’Baibo wokamba za nthawi imene tikukhalamo, yomwe imachedwa “cimalizilo ca nthawi ino.”—Mateyu 24:3.

  •   “Mudzamva phokoso la nkhondo komanso mbili za nkhondo. . . . Mtundu udzaukilana na mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana na ufumu wina.”​—Mateyu 24:6, 7.

 Ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi “ya Mapeto” N’chiyani?’” kuti muone mmene nkhondo zikukwanilitsila ulosi wa m’Baibo.

Nkhondo imene idzathetsa nkhondo zonse

 Baibo inakambilatu kuti nkhondo zidzatha. Zimenezi zidzatheka osati na mphamvu za anthu koma na nkhondo ya Aramagedo, imene ni “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Nkhondoyi ikadzatha, Mulungu adzakwanilitsa zimene analonjeza zakuti anthu adzasangalala na mtendele wosatha.—Salimo 37:10, 11, 29.

 Kuti mudziŵe zambili za nkhondo ya Mulungu imene idzathetsa nkhondo zonse, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo N’ciyani?

a Lipoti la mu January 2024, la bungwe lochedwa ACLED Conflict Index, “Loonetsa kufalikila na kukula kwa zaciwawa padziko lonse”