Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Baibo Imathandiza Bwanji Anthu Kukhala Ololela?

Kodi Baibo Imathandiza Bwanji Anthu Kukhala Ololela?

 “Kulolelana [ni] khalidwe lofunika kwambili kuti padziko pakhale mtendele.”—Inatelo UNESCO Declaration of Principles on Tolerance, ya mu 1995.

 Kumbali ina, kusalolelana kungapangitse anthu kukhala opanda ulemu komanso kudana. Khalidwe limeneli likakula msinkhu, anthu amayamba kulankhulana mawu acipongwe, kusankhana mitundu komanso zaciwawa.

 Koma nkhani ya kulolelana anthu amaiona mosiyana-siyana. Ena amakhulupilila kuti munthu wololela ayenela kuvomeleza makhalidwe a mtundu uliwonse. Koma ena amagwilizana na zimene Baibo imakamba, zakuti munthu wololela amalemekeza ufulu wa munthu aliyense komanso zimene amakhulupilila. Amacita zimenezi ngakhale kuti iwo eni sagwilizana nawo makhalidwewo kapena zikhulupililo zimenezo.

 Kodi Baibo ingathandizedi anthu kukhala ololela masiku ano?

Zifukwa za m’Baibo Zokhalila Wololela

 Baibo imalimbikitsa khalidwe la kulolelana. Imati: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololela.” (Afilipi 4:5) Baibo imatilimbikitsa kuti tizicita zinthu na anthu ena mowaganizila, mwaulemu, ndiponso mwacilungamo. Aja omwe amatsatila malangizowa, mwina sangagwilizane kapena kutengela makhalidwe a wina wake, koma amalola munthuyo kucita zinthu malinga na cisankho cake.

 Komabe, Baibo imaonetsa kuti pali makhalidwe ena amene Mulungu amavomeleza. Imati: “Iwe munthu wocokela kufumbi, [Mulungu] anakuuza zimene zili zabwino.” (Mika 6:8) Imaonetsa malangizo a Mulungu kwa anthu, owathandiza kukondwela na umoyo wabwino koposa.—Yesaya 48:17, 18.

 Mulungu satilola kuweluza ena. Malinga n’kunena kwa Baibo, “wopeleka lamulo ndi woweluza alipo mmodzi yekha. . . . Ndiwe ndani, kuti uziweluza mnzako?” (Yakobo 4:12) Mulungu amapatsa aliyense wa ife ufulu wopanga zisankho, ndipo zotulukapo zake zimakhala mlandu wathu.—Deuteronomo 30:19.

Zimene Baibo imakamba pa nkhani ya kupatsana ulemu

 Baibo imati tiyenela kucitila “ulemu anthu onse.” (1 Petulo 2:17, Buku Lopatulika) Conco, aja omwe amayendela mfundo za m’Baibo amalemekeza anthu onse, mosayang’ana zimene amakhulupilila kapena zisankho zawo. (Luka 6:31) Izi sizitanthauza kuti amene amatsatila Baibo azingovomeleza zilizonse zimene anthu amakamba kapena kukhulupilila ayi, kapena kumangovomeleza zisankho zilizonse zimene ena angapange ayinso. Koma m’malo mocita zinthu mwaukali komanso mopanda ulemu, iwo amayesetsa kutengela mmene Yesu anali kucitila zinthu na anthu.

 Mwacitsanzo, nthawi ina Yesu anakumana ni mayi amene anali wacipembedzo comwe iye sanali kugwilizana naco. Cinanso, mayiyu anali kukhala na mwamuna amene sanali wake—khalidwe limene Yesu sanali kuliyanja. Ngakhale n’telo, iye analankhula naye mwaulemu.—Yohane 4:9, 17-24.

 Potengela Yesu, Akhristu amakhala okonzeka kufotokoza zimene amakhulupilila kwa aliyense wofuna kumvetsela, ndipo amacita zimenezo “mwaulemu kwambili.” (1 Petulo 3:15) Baibo imalangiza Akhristu kusakakamiza anthu ena kuyendela maganizo awo. Imakamba kuti wotsatila wa Khristu “sayenela kukangana ndi anthu, koma ayenela kukhala wodekha kwa onse,” kuphatikizapo a zipembedzo zina.—2 Timoteyo 2:24.

Kodi Baibo imatipo ciyani pa nkhani ya cidani

 Baibo imatilimbikitsa “kukhala pa mtendele ndi anthu onse.” (Aheberi 12:14) Munthu wolimbikitsa mtendele amapewa cidani. Mosacita kufika polakwila cikumbutima cake, iye amayesetsa kucita zonse zotheka kuti akhale pa mtendele na ena. (Mateyu 5:9) Ndiye cifukwa cake Baibo imalimbikitsanso Akhristu kukonda adani awo pocita mokoma mtima kwa anthu owacita zoipa.—Mateyu 5:44.

 N’zoona kuti Baibo imati Mulungu “amadana,” kapena “kunyansidwa,” na makhalidwe amene amacotsela anthu ulemu kapena kuvulaza ena. (Miyambo 6:16-19) Koma apa Baibo yaseŵenzetsa liwu lakuti “kudana” pofotokoza kukhudzidwa mtima kwambili na makhalidwe oipa. Baibo imaonetsa kuti Mulungu ni wokonzeka kukhululuka na kuthandiza anthu amene afuna kusintha zocita zawo kuti akhale ni umoyo wogwilizana na miyeso yake.—Yesaya 55:7.

Mavesi a m’Baibo okamba za kulolela komanso ulemu

 Tito 3:2: “Akhale ololela, ndi ofatsa kwa anthu onse.”

 Munthu wololela amamvetsela mofatsa malingalilo osiyana-siyana, komanso amalemekeza anthu onse.

 Mateyu 7:12: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.”

 Tonsefe timakondwela anthu ena akamacita nafe mwaulemu komanso zoonetsa kuti amalemekeza maganizo athu na mmene tikumvela. Kuti mudziŵe zambili za mogwilitsila nchito lamulo la makhalidwe abwino limene Yesu anaphunzitsa, onani nkhani ya mutu wakuti “Kodi Yesu Anapereka Lamulo Lotani Lokhudza Kuchita Zinthu ndi Ena?

 Yoswa 24:15: “Sankhani lelo amene mukufuna kum’tumikila.”

 Tikamalemekeza ufulu wa ena wodzisankhila zocita, timalimbikitsa mtendele.

 Machitidwe 10:34: “Mulungu alibe tsankho.”

 Mulungu sasankha munthu aliyense potengela mtundu wake, zakuti ni mkazi kapena mwamuna, dziko, cikhalidwe, kaya zakuti ni wolemela kapena wosauka ayi. Awo amene afuna kutengela makhalidwe a Mulungu amalemekeza anthu onse.

 Habakuku 1:12, 13: ‘[Mulungu] sangathe kuonelela khalidwe loipa.’

 Kulolela kwa Mulungu kuli na polekezela pake. Iye sadzalekelela khalidwe loipa la anthu kupitiliza mpaka kale-kale ayi. Kuti mudziŵe zambili, onelelani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

 Aroma 12:19: “Siyilani malo mkwiyo wa Mulungu. Pakuti malemba amati: ‘Kubwezela ndi kwanga, ndidzawabwezela ndine,’ watelo Yehova.” a

 Yehova Mulungu savomeleza munthu aliyense kubwezela. Iye adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika pa nthawi yake yoikika. Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani ya pa webusaiti yakuti, “Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?

a Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?