KHALANI MASO!
Kutentha Koopsa pa Dziko Lonse mu 2023—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Anthu pa dziko lonse akuvutika na kutentha koopsa kumene sikunacitikepo n’kale lonse. Akulimbananso na matsoka obwela cifukwa ca kutenthaku. Onani malipoti otsatilawa:
“Pa zaka 174 zimene anthu akhala akupima nyengo, dziko lapansi lisanatenthepo ngati mmene linatenthela caka cino m’mwezi wa June.”—Inatelo lipoti ya National Oceanic and Atmospheric Administration, U.S. Department of Commerce, ya pa July 13, 2023.
“Ku Italy, Spain, France, Germany na Poland kukutentha kwambili. Ndipo anthu akuyembekezela kuti pa zilumba za Sicily na Sardinia padzatentha kwambili mpaka kufika madigiri 48. Aka n’koyamba nyengo kutentha kwambili conco ku Europe.”—Inatelo lipoti ya European Space Agency, ya pa July 13, 2023.
“Popeza dziko lapansi likutentha kwambili, tikuyembekezela kuti mvula yoopsa izigwa kawili-kawili. Izi zidzapangitsa kuti vuto la kusefukila kwa madzi likule kwambili.”—Anatelo Stefan Uhlenbrook, mkulu wa nthambi yoona za madzi na nyengo ya m’bungwe la World Meteorological Organization, pa July 17, 2023.
Kodi mumada nkhawa mukaona kuculuka kwa malipoti okamba za kusokonezeka kwa nyengo? Onani zimene Baibo imakambapo pa nkhani yofunika imeneyi.
Kodi kusintha kwa nyengo kukukwanilitsa ulosi wa m’Baibo?
Inde. Kutentha koopsa pa dziko lonse na zocitika zina zokhudza kusokonezeka kwa nyengo, zigwilizana ni zimene Baibo inakambilatu kuti zidzacitika m’masiku athu ano. Mwacitsanzo, Yesu analosela kuti “kudzaoneka zoopsa,” kapena kuti zinthu zochititsa mantha. (Luka 21:11) Kutentha koopsa kumeneku kwapangitsa anthu ambili kukhala na nkhawa yakuti anthu adzaliwononga kothelatu dzikoli.
Kodi dziko lapansi lidzawonongeka kothelatu?
Ayi. Mulungu analenga dziko lapansi kuti tikhalemo kwamuyaya. Iye sadzalola kuti anthu aliwononge kothelatu. (Salimo 115:16; Mlaliki 1:4) Ndipo analonjeza kuti adzawononga “amene akuwononga dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:18.
Baibo imaonetsa kuti Mulungu ali na mphamvu zoteteza dzikoli kuti lisawonongeke kothelatu, ndipo adzacitadi zimenezi.
“[Mulungu] amacititsa mphepo yamkuntho kukhala bata, moti mafunde a panyanja amadekha.” (Salimo 107:29) Mulungu ali na mphamvu zolamulila mphamvu za m’cilengedwe. Iye alinso na mphamvu zothetsa mavuto a zacilengedwe omwe akucititsa kuti anthu azivutika na matsoka a zacilengedwe.
Malemba amati: “Inu mwatembenukila dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zoculuka, mwalilemeletsa kwambili.” (Salimo 65:9) Yehova adzadalitsa anthu, ndipo dziko lidzakhala paradaiso.
Kuti muphunzile zambili zokhudza lonjezo la m’Baibo lakuti Mulungu adzathetsa mavuto a zacilengedwe, onani nkhani yakuti “Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?”