Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yan Zabolotnyi/stock.adobe.com

KHALANI MASO!

Kuwonjezeka kwa Kusamvela Malamulo Padziko Lonse—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Kuwonjezeka kwa Kusamvela Malamulo Padziko Lonse—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Ku Haiti magulu a zigawenga akucita zaciwawa pa mlingo wodetsa nkhawa. Ku South Africa, ku Mexico komanso ku Latin America kukucitika zaciwawa zimene zabweletsa mavuto ambili. Ngakhale ku madela kumene zaciwawa zacepekela, anthu amakhalabe na nkhawa komanso amaona kuti ni osatetezeka akamva malipoti akuti katundu wabedwa, wawonongedwa kapena watenthedwa.

 Kodi Baibo ikutipo ciyani pa kusamvela malamulo kumene kukucitika padziko lonse?

Zimene Baibo inakambilatu pa nkhani ya kusamvela malamulo

 Baibo inanenelatu kuti kusamvela malamulo kudzakhala mbali ya cizindikilo ca “cimalizilo ca nthawi ino.” (Mateyo 24:3) Pofotokoza zocitika zimene zili mbali ya cizindikiloci, Yesu anati:

  •   “Ndiponso cifukwa ca kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzacepa.”—Mateyo 24:12.

 Baibo inakambilatunso kuti ‘m’masiku otsiliza’ anthu adzakhala “osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino.” (2 Timoteyo 3:1-5) Makhalidwe oonetsa kudzikonda amenewa amapangitsa kusamvela malamulo kumene timaona masiku ano.

 Koma tili na zifukwa zokhalila na ciyembekezo. Baibo imalonjeza kuti posacedwapa kusamvela malamulo kudzatha.

  •   “Kwatsala kanthawi kocepa, ndipo oipa sadzakhalaponso. Udzayangʼana pamene ankakhala, Ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:10, 11.

 Dziŵani zambili ponena za uthenga wa m’Baibo wa ciyembekezo komanso cifukwa cake mungakhale otsimikiza kuti zimene zikucitika masiku ano zikukwanilitsa maulosi a m’Baibo. Ŵelengani nkhani zotsatilazi.

 Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo

 Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi “ya Mapeto” N’chiyani?

 Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?