Kodi Baibo Imatipo Ciyani pa Kusoŵa kwa Cakudya?
“Kutsiliza njala.” Izi n’zimene atsogoleli a maiko amafuna. Iwo amafuna kupeza njila yothandiza anthu onse padziko kukhala na cakudya cokwanila. Koma kodi njala ingathe padziko? a Kodi Baibo imakambapo ciyani?
Baibo inakambilatu za kusoŵa kwa cakudya kumene timakuona
Baibo inanenelatu kuti m’masiku athu ano kudzakhala kusoŵa kwa cakudya. Imacha nthawiyi kuti “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1) Mulungu si ndiye amacititsa kusoŵa kwa cakudya, koma anaticenjeza za vutoli. (Yakobo 1:13) Onani maulosi a m’Baibo aŵiliwa.
“Kudzakhala njala . . . m’malo osiyana-siyana.” (Mateyu 24:7) Ulosi wa m’Baibo umenewu unakambilatu kuti kudzakhala njala m’malo ambili. N’zocititsa cidwi kuti lipoti laposacedwa locokela kwa anthu oona pa kapangidwe kacakudya linati: “Njala ya padziko lonse, komanso kusoŵa kwa cakudya copatsa thanzi kukuwonjezeleka.” b Anthu mamiliyoni ambili m’maiko oculuka sakwanitsa kupeza cakudya cokwanila. N’zomvetsa cisoni kuti, cifukwa ca izi, ambili mwa anthu amenewa amamwalila.
“Ndinaona hachi yakuda. Wokwelapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake.” (Chivumbulutso 6:5) Mu ulosi umenewu, hachi yophipilitsa komanso wokwelapo wake akuimila njala m’masiku ano otsiliza. c Masikelo omwe ali m’dzanja la wokwela pa hachiyo ni oyezela cakudya kuti munthu aliyense alandileko zocepa. Pomwe wokwela pa hachiyo akuyenda, kukumveka mawu onena kuti mtengo wa cakudya udzakwela kwambili, ndipo akucenjeza anthu kuti asawononge cakudya cimene ali naco. (Chivumbulutso 6:6) Izi zionetsa bwino kucepekela kwa cakudya padziko lonse masiku ano, cifukwa anthu mabiliyoni ambili sakwanitsa kupeza cakudya copatsa thanzi.
Mmene Vuto la Njala Lidzathele
Akatswili amati dziko lapansi limatulutsa cakudya cambili cokwanila kudyetsa anthu onse padziko. Ndiye, kodi n’ciyani cimapangitsa kuti cakudya cizisoŵa? Kodi Baibo imati Mlengi wathu, Yehova, d adzacitapo ciyani kuti acotsepo mavutowa?
Vuto: Maboma sangathetse umphawi komanso mavuto a zacuma amene amabweletsa njala.
Mmene Lidzathele: Maboma a anthu adzalowedwa m’malo na boma labwino, limene ni Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Masiku ano anthu osauka ambili amavutika kupeza cakudya. Koma mu ulamulilo wa Mulungu zimenezi zidzatha. Pokamba za Yesu Khristu, Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Baibo imati: “Pakuti adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. . . . Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.”—Salimo 72:12, 16.
Vuto: Nkhondo zimawononga zinthu na kubweletsa mavuto a zacuma m’dziko, zimene zimapangitsa kuti anthu alephele kupeza cakudya.
Mmene Lidzathele: “[Yehova] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.” (Salimo 46:9) Mulungu adzawononga zida za nkhondo komanso anthu amene amacititsa nkhondo. Izi zidzathandiza kuti aliyense azipeza cakudya mosavuta. Baibo imalonjeza kuti: “Wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendele woculuka.”—Salimo 72:7.
Vuto: Nyengo yoopsa na matsoka azacilengedwe amawononga mbewu na kupha ziweto.
Mmene Lidzathele: Mulungu adzalamulila mphamvu zacilengedwe, ndipo adzacititsa kuti nyengo ikhale yabwino kubyalamo cakudya. Baibo imati: “[Yehova] amacititsa mphepo yamkuntho kukhala bata, moti mafunde a panyanja amadekha. . . . Amasandutsa cipululu kukhala dambo la madzi, Ndipo dziko lopanda madzi amalisintha kukhala dela la akasupe amadzi. Kumeneko amakhazikako anthu anjala . . . Anthuwo amafesa mbewu ndi kulima minda ya mpesa, kuti akhale ndi zokolola.”—Salimo 107:29, 35-37.
Vuto: Anthu adyela komanso acinyengo amapanga zakudya zimene si zabwino kudya, kapena amapangitsa kuti anthu alephele kupeza cakudya cofunikila.
Mmene Lidzathele: Ufumu wa Mulungu udzacotsapo anthu onse acinyengo komanso aziphuphu. (Salimo 37:10, 11; Yesaya 61:8) Pokamba za Yehova Mulungu, Baibo imati “iye ndi Wopelekela ciweluzo anthu ocitilidwa cinyengo, Wopeleka cakudya kwa anthu anjala.”—Salimo 146:7.
Vuto: Cakudya cambili padziko lonse cimawonongedwa kapena kutayidwa caka ciliconse.
Mmene Lidzathele: Mu Ufumu wa Mulungu, anthu adzayamba kusamalila bwino cakudya. Ali pa dziko lapansi, Yesu anapewa kuwononga cakudya. Mwacitsanzo, pa nthawi ina iye anadyetsa anthu oposa 5,000. Pambuyo pake, anauza ophunzila ake kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke ciliconse.”—Yohane 6:5-13.
Popeza Ufumu wa Mulungu udzacotsapo mavuto amene amabweletsa njala, anthu onse adzakondwela kukhala na cakudya coculuka, copatsa thanzi. (Yesaya 25:6) Kuti mudziŵe mmene Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsile zimenezi, onani nkhani yakuti “Nanga Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulila Dziko Lapansi?”
a Pulogilamu Yokhala na Cakudya Cokwanila mu 2030, yovomelezedwa na Maiko Ogwilizana na Bungwe la United Nations mu 2015.
b Lipoti locokela ku mabungwe a Food and Agriculture Organization of the United Nations, International Fund for Agricultural Development, United Nations Children’s Fund, United Nations World Food Programme, komanso World Health Organization.
c Kuti mudziŵe zambili za amuna anayi okwela pa mahosi, onani nkhani yakuti “Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?”
d Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”