Mavuto a Zaumoyo—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacitapo Ciyani?
“COVID-19 silinso mlili wosakadza padziko muja zinalili kumbuyoku. Koma sizitanthauza kuti ciopsezo ca COVID-19 padziko lonse cathelatu iyayi. . . Tifuna kuti mlili wina ukadzabwela—cifukwa udzabwela ndithu—udzatipeze titaukonzekela pasadakhale.”—Anatelo, Dr. Tedros Adhanom Ghebreyesus, mkulu wa bungwe la World Health Organization, pa May 22, 2023.
Anthu ambili omwe anadwalapo matenda a COVID-19, akuvutikabe na mavuto ena okhudza thanzi, komanso matenda a maganizo. Kodi maboma komanso a zaumoyo adzakhala ataukonzekela mokwanila mlili wotsatila ukadzafika? Nanga matenda amene tikuvutika nawo pali pano angathe kuwacotsapo?
Baibo imakamba za boma limene lidzapeleke cisamalilo comwe tikufunikila pa nkhani ya zaumoyo. Imati, “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu,” kapena kuti boma. (Danieli 2:44) Ufumuwo ukadzayamba kulamulila, ‘palibe wokhalamo amene adzanene kuti nadwala.’ (Yesaya 33:24) Munthu alliyense adzasangalala na thanzi labwino, komanso adzakhala wamphamvu ngati mnyamata.—Yobu 33:25.