Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kumanzele: Olena Yefremkina/stock.adobe.com; center: lunamarina/stock.adobe.com; right: Rido/stock.adobe.com

KHALANI MASO!

Ndani Amene Mungadalile?—Kodi Baibulo Ikutipo Ciyani?

Ndani Amene Mungadalile?—Kodi Baibulo Ikutipo Ciyani?

 Anthu amakhumudwa ngati anthu omwe amawakhulupilila awagwilitsa mwala. Ambili analeka kukhulupilila . . .

  •   atsogoleli andale amene amaika zofuna zawo patsogolo m’malo mwa zofunikila za anthu amene akuwatsogolela.

  •   mabungwe ofalitsa nkhani amene amalephela kufalitsa nkhani mwacilungamo komanso molondola.

  •   asayansi amene amacita zinthu zopindulila iwo m’malo mwa zopindulitsa anthu ambili.

  •   atsogoleli azipembedzo amene amatengako mbali kwambili m’zandale m’malo moimilako Mulungu.

 M’pomveka kuti anthu amakhala osamala poona anthu amene angakhulupilile. Baibulo limacenjeza kuti:

  •   “Musamakhulupilila zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe cipulumutso mwa iye.”—Salimo 146:3, Buku Lopatulika.

Munthu amene mungakhulupilile

  Baibulo limakamba za munthu amene mungakhulupilile, munthuyo ndi Yesu Khristu. Sanali cabe munthu wabwino amene anakhalako zaka zambili kumbuyoku. Mulungu anasankha Yesu kuti ‘adzalamulile monga Mfumu . . . , ndipo Ufumu wake sudzatha.’ (Luka 1:32, 33) Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, boma limene palipano likulamulila kucokela kumwamba.—Mateyo 6:10.