Nkhondo—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacitapo Ciyani?
Zungulile dziko lapansi, nkhondo zikupitilizabe ndipo zikusakaza zinthu, miyoyo ya anthu, na kubweletsa mavuto ambilimbili. Tamvelani malipoti awa:
“Ziŵelengelo zionetsa kuti anthu ambili anamwalila pa nkhondo caka catha, kuposa m’zaka 28 zapitazo. Zili conco maka-maka cifukwa ca nkhondo ya ku Ethiopia na ku Ukraine.”—Inatelo bungwe la Peace Research Institute Oslo, ya June 7, 2023.
“Nkhondo ya ku Ukraine ni imodzi mwa nkhondo zimene zinawononga kwambili mu 2022. Caka catha, ciwawa cocitika cifukwa ca ndale cinawonjezeka na 27% pa dziko lonse. Ndipo anthu pafupi-fupi 1.7 biliyoni anakhudzidwa.”—Inatelo bungwe la The Armed Conflict Location & Event Data Project (ACLED), ya February 8, 2023.
Baibo imatipatsa ciyembekezo. Imakamba kuti “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.” (Danieli 2:44) Ufumuwo kapena kuti bomalo likadzayamba kulamulila, Mulungu adzathetsa “nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—Salimo 46:9.