Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Sean Gladwell/Moment via Getty Images

KHALANI MASO!

Ndalama Zopitilila $2 Tililiyoni Zawonongedwa pa Zida Zankhondo—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Ndalama Zopitilila $2 Tililiyoni Zawonongedwa pa Zida Zankhondo—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Mu 2022, maboma padziko lonse anaseŵenzetsa ndalama zopitilila madola 2.24 tililiyoni a ku America, maka-maka cifukwa ca nkhondo ya pakati pa dziko la Russia na Ukraine. Malinga na lipoti la mu April 2023, limene bungwe la Stockholm International Peace Research Institute (SIPRI) linatulutsa, linati mu 2022:

  •   Ndalama zimene maiko a ku Europe anawonongela pa zankhondo “zinawonjezeka na 13 pelesenti pa caka. Ici n’ciŵelengelo cacikulu kwambili kuposa ndalama zonse zimene maboma a ku Europe anagwilitsa nchito kucokela pa nkhondo yolimbana na mawu okha mu 1991.”

  •   “Ciŵelengelo ca ndalama zimene dziko la Russia linaseŵenzetsa cinawonjezeka na pafupifupi 9.2 pelesenti. Izi zapangitsa kuti dzikoli licoke pa nambala 5 n’kukhala lacitatu pa maiko amene akuseŵenzetsa ndalama zambili padziko lonse.”

  •   Dziko la America ndilo limagwilitsa nchito ndalama zoculuka kuposa maiko onse. “Iwo anaseŵenzetsa ndalama zokwana 39 pelesenti polinganiza na zimene maiko ena anagwilitsa nchito.”

 “Kuwilikizika kumeneku kowonongela ndalama zambili-mbili pa zankhondo m’zaka zaposacedwazi, kukuonetsa kuti tikukhala m’dziko limene citetezo kwa anthu cikucepela-cepela.” Anatelo Dr. Nan Tian, waciŵili kwa wolemba lipoti la SIPRI.

 Baibo inakambilatu kuti kukangana pakati pa maulamulilo amphamvu padziko lonse kudzawonjezeka, komanso imatiuza cimene cingabweletse mtendele weniweni.

Kuwonjezeka kwa Nkhondo Kukukwanilitsa Ulosi

  •   Baibo imacha masiku amene tikukhalamo kuti “nthawi ya mapeto.”Danieli 8:19.

  •   Buku la Danieli linanenelatu kuti pa nthawiyo, maulamulilo amphamvu padziko lonse adzakangana. Maulamulilo amphamvu amenewa, ‘adzakankhana’ kapena kulimbilana ulamulilo. Kukankhana kumeneku kudzacititsa kuti awononge “cuma” coculuka.—Danieli 11:40, 42, 43.

 Kuti mudziŵe zambili za ulosi wa m’Baibo wocititsa cidwi umenewu, onelelani vidiyo ya mutu wakuti Kukwanilitsika kwa Maulosi a pa Danieli Caputala 11.

Mmene mtendele weniweni udzabwelela

  •   Baibo imati Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo maufumu onse a anthu. Imati iye “adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.

  •   Posacedwa, Yehova a Mulungu adzacita zimene anthu sangakwanitse kucita—adzabweletsa mtendele weniweni komanso wosatha. Motani? Ufumu wake, umene ni boma lakumwamba, udzacotsapo zida zonse zakhondo na kuthetsa ciwawa conse.—Salimo 46:8, 9.

 Kuti mudziŵe zambili zimene Ufumu wa Mulungu udzacita, ŵelengani nkhani yakuti “Mu Ufumu wa Mulungu, pa Dziko ‘Padzakhala Mtendele Woculuka.’

a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.