Zimene Baibo Ikambapo pa Kukula kwa Vuto la Kusoŵa Woceza Naye
Malinga na lipoti la posacedwa la padziko lonse, a pafupifupi munthu mmodzi pa anthu 4 alionse amasoŵa woceza naye.
“Vuto la kusoŵa woceza naye lingakhudze munthu aliyense, mosasamala kanthu za msinkhu wake kapena kumene amakhala.”—Anatelo Chido Mpemba, waciŵili kwa wakumpando m’bungwe la World Health Organization’s Commission on Social Connection.
Anthu ambili amaganiza kuti anthu okalamba komanso amene amakhala kutali na anthu ena ni amene amasungulumwa. Koma zoona zake n’zakuti ngakhale acinyamata, anthu a thanzi labwino, ocita bwino pa umoyo, komanso okwatila, nawonso amasungulumwa nthawi zina. Vuto la kusoŵa woceza naye lingabweletse mavuto a kuthupi komanso a maganizo.
“Dokotala wina wa ku America, dzina lake Vivek Murthy anati: “Kusungulumwa ni vuto lalikulu ndipo si kukhala cabe wokhumudwa kapena kumvela kuipa.” Anakambanso kuti “munthu amene amasoŵa woceza naye, moyo wake umakhala pa ciopsezo cacikulu mofanana na munthu amene amakoka ndudu 15 za fodya tsiku lililonse.”
Zimene Baibo imakamba
Mlengi wathu safuna kuti tizisoŵa woceza naye. Kucokela pa ciyambi, cifunilo ca Mulungu n’cakuti anthu azisangalala na mabwenzi abwino.
Mfundo ya m’Baibo: “Mulungu anati: ‘Si bwino kuti munthu azikhala yekha.’”—Genesis 2:18.
Mulungu afuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. Iye analonjeza kuti adzatiyandikila ngati tiyesetsa kumuyandikila.—Yakobo 4:8.
Mfundo ya m’Baibo: “Osangalala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu cifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo.”—Mateyu 5:3.
Mulungu amafuna kuti tizimulambila pamodzi na anthu ena. Tikamacita zimenezi timakhala acimwemwe.
Mfundo ya m’Baibo: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana cikondi ndiponso kucita zabwino. Tisasiye kusonkhana pamodzi, . . . koma tiyeni tilimbikitsane.”—Aheberi 10:24, 25.
Kuti mudziŵe cifukwa cake kuthetsa vuto la kusungulumwa n’kofunika, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Mungacite Ciyani Ngati Mumasoŵa Woceza Naye?.”
a The Global State of Social Connections, by Meta and Gallup, 2023.