Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KHALANIBE MASO!

Zimene Zipembedzo Zikucita pa Nkhondo ya ku Ukraine—Kodi Baibo Imati Ciyani?

Zimene Zipembedzo Zikucita pa Nkhondo ya ku Ukraine—Kodi Baibo Imati Ciyani?

 Mvelani zimene atsogoleli ochuka a zipembedzo akucita pa nkhondo ya ku Ukraine:

  •   “Mkulu wa chalichi ca Russian Orthodox, wochedwa Patriarch Kirill, sanakambepo ciliconse codzudzula boma la Russia pa nkhondo imeneyi. . . . Zabodza zimene Chalichi yawo ikufalitsa zapatsa mphamvu Putin kuti azilungamitsa nkhondo imene akuthila dziko la Ukraine.”—Nyuzipepala ya EUobserver, March 7, 2022.

  •   “Patriarch Kirill . . . wanena mawu olungamitsa nkhondo imene dziko lake likuthila dziko la Ukraine—wati nkhondoyi ni njila imodzi yothana na ucimo.”—AP News, March 8, 2022.

  •   “Mtsogoleli wa Orthodox Church ku Ukraine, wochedwa Metropolitan Epiphanius I wa ku Kyiv, pa Mande anadalitsa anthu ake kuti ‘akamenyane na adani a ku Russia amene aloŵelela m’dziko lawo’ . . . [Iye] anatinso kupha asilikali a ku Russia si chimo iyayi.”—Jerusalem Post, March 16, 2022.

  •   “Ife a bungwe la [Ukrainian Council of Churches and Religious Organizations (UCCRO)] tili pamodzi na asilikali a Ukraine komanso onse amene akutithandiza pa nkhondoyi. Komanso onsewo tikuwadalitsa polimbana na adani athuwo kuti ateteze dziko la Ukraine, ndipo tikuwapemphelela.”—Mawu a bungwe la UCCRO a, February 24, 2022.

 Kodi inuyo muganiza bwanji? Popeza zipembedzo zimati zimatsatila Yesu Khrisu, kodi n’cinthu coyenela kulimbikitsa anthu awo kukamenya nkhondo? Nanga Baibo imakamba ciyani?

Mmene zipembedzo zacitila pa nkhondo m’mbili ya anthu

 M’mbili yonse ya anthu, kaŵili-kaŵili zipembedzo zalekelela nkhondo zikucitika, zazilungamitsa, ngakhale kulimbikitsa kuti zicitike, koma kwinaku zikunamizila kuti zikusungitsa mtendele. Kwa zaka zambili, a Mboni za Yehova avumbulutsa poyela cinyengo ca zipembedzo cimeneci. Nazi zitsanzo zina zochulidwa m’zofalitsa zathu.

  •   Nkhani ya m’Cizungu yakuti “The Crusades—A ‘Tragic Illusion” ionetsa mmene Chalichi ca Katolika cinatengelapo gawo pa kuphedwa kwa anthu ambili-mbili amene anaphedwa m’dzina la Mulungu na Khristu.

  •   Nkhani yakuti “Tchalitchi cha Katolika mu Afirika” inafotokoza mmene zipembedzo zinalephelela kuletsa nkhodo ya pakati pa mitundu, ngakhale yofuna kupulula mtundu wonse.

  •   Nkhani zakuti “Kodi Zipembedzo N’zimene Zikusokoneza Mtendere?,” “Mbali ya Chipembedzo m’Nkhondo za Anthu,” komanso yakuti, “Chipembedzo Chichirikiza Mbali Ina,” zimafotokoza mmene atsogoleli a Chalichi ca Katolika, Orthodox, komanso Cipulotesitanti, athandizila mbali zonse zolimbana pa nkhondo zambili.

Kodi machalichi ayenela kutengapo mbali pa nkhondo?

 Yesu anaphunzitsa kuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mateyu 22:39) “Pitilizani kukonda adani anu.”—Mateyu 5:44-47.

 Ganizilani izi: Kodi tinganene kuti cipembedzo cimamvela malamulo a Yesu onena za kukondana ngati cilimbikitsa mamembala ake kupha anthu pa nkhondo? Kuti mupeze yankho, ŵelengani nkhani yakuti “Akhristu Oona Ndi Nkhondo” komanso yakuti “Kodi Nzotheka-Kukonda Adani Athu?

 Yesu anakamba kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisapelekedwe.” (Yohane 18:36) “Onse ogwila lupanga adzafa ndi lupanga.”—Mateyu 26:47-52.

 Ganizilani izi: Popeza Akhristu sanaloledwe kucita nkhondo, ngakhale pofuna kuteteza Yesu, kodi pangakhale cifukwa comveka cotengelako mbali pa nkhondo? Kuti muone mmene Akhristu oyambilila anatsatilila mokhulupilika citsanzo ca Yesu komanso zimene iye anaphunzitsa, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?

Kodi n’ciyani cidzacitikila zipembedzo zimene zimalimbikitsa nkhondo?

 Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu savomeleza zipembedzo zimene zimangonena m’pakamwa kuti zimaimilako Yesu, koma sizitsatila zimene iye anaphunzitsa.—Mateyu 7:21-23; Tito 1:16.

  •   Buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti zipembedzo zotelozo zili na mlandu wa imfa za “onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 18:21, 24) Kuti mudziŵe cifukwa cake, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?

  •   Yesu pofotokoza kuti “mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino amaudula ndi kuuponya pamoto,” anaonetsa kuti zipembedzo zonse zimene Mulungu sazivomeleza zidzawonongedwa cifukwa ca nchito zawo zoipa. (Mateyu 7:15-20) Kuti mudziŵe mmene izi zidzacitikila, ŵelengani nkhani yakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!

Photo credits, left to right: Photo by Sefa Karacan/Anadolu Agency/Getty Images; Maxym Marusenko/NurPhoto via Getty Images

a Mu Bungwe la UCCRO, kutanthauza Ukrainian Council of Churches and Religious Organizations, muli machalichi 15 oimilako mipingo ya Orthodox, Greek na Roman Catholic, Protestant, na Evangelical, kuphatikizaponso Ayuda komanso Asilamu.