NYIMBO 148
Yehova Amapulumutsa
(2 Samueli 22:1-8)
-
1. Yehova, ndimwedi Mulungu wamoyo;
Ndimwe munalenga
kumwamba na dziko.
Ndani angalimbane namwe M’lungu?
Kulibe.
Adani adziŵe.
(KOLASI)
Yehova M’lungu wathu m’pothaŵila.
Iye ni Thanthwe kwa atumiki ake.
Tisayope, tilimbe mtima.
Dzina lake tilengeze pa dziko lonse,
tim’tamande.
-
2. Ngakhale kuti nizingidwe na imfa,
Atate Yehova,
nipatseni mphamvu.
Nilimbitseni mtima,
n’tetezeni,
Nipempha, conde M’lungu wanga.
(KOLASI)
Yehova M’lungu wathu m’pothaŵila.
Iye ni Thanthwe kwa atumiki ake.
Tisayope, tilimbe mtima.
Dzina lake tilengeze pa dziko lonse,
tim’tamande.
-
3. Kucokela kumwamba mudzabangula.
Olimbana namwe
adzati nje nje nje.
Koma okukondani
adzakondwa
Cifukwa adzapulumuka.
(KOLASI)
Yehova M’lungu wathu m’pothaŵila.
Iye ni Thanthwe kwa atumiki ake.
Tisayope, tilimbe mtima.
Dzina lake tilengeze pa dziko lonse,
tim’tamande.
(Onaninso Sal. 18:1, 2; 144:1, 2.)