NYIMBO 7
Yehova Ndiye Mphamvu Zathu
(Yesaya 12:2)
-
1. M’lungu wathu ndimwe mphamvu zathu.
Imwe ndimwe mpulumutsi wathu.
Timalengeza uthenga wanu,
Ngakhale kuti ena samvela.
(KOLASI)
Yehova ndimwe wamphamvuzonse.
Timadziŵitsa dzina lanu.
Yehova timakudalilani.
Ndimwe mphamvu zathu—nsanja yathu.
-
2. Mwationetsa kuwala kwanu.
M’lungu mwatiphunzitsa co’nadi.
Mu Mau anu tipeza nzelu;
Ise tasankha Ufumu wanu.
(KOLASI)
Yehova ndimwe wamphamvuzonse.
Timadziŵitsa dzina lanu.
Yehova timakudalilani.
Ndimwe mphamvu zathu—nsanja yathu.
-
3. Timatumikila mokondwela,
Ngakhale Satana ‘tivutitse.
Ngakhale tikumane na imfa
Ise tidzamvela imwe cabe.
(KOLASI)
Yehova ndimwe wamphamvuzonse.
Timadziŵitsa dzina lanu.
Yehova timakudalilani.
Ndimwe mphamvu zathu—nsanja yathu.
(Onaninso 2 Sam. 22:3; Sal. 18:2; Yes. 43:12.)