Kumanga Tsogolo Langa na Yehova
Daunilodi:
1. Sembe ningakwanitse kudziŵa za tsogolo langa,
Ningadziŵe mmene umoyo wanga udzakhalila.
Ine nidziŵa, olo zivute bwanji
Nipeleka moyo wanga kwa M’lungu.
(KOLASI)
Pa zonse nili nazo pa umoyo wanga,
Coposa zonse, inde capadela
Nikukondweletsa M’lungu mwa zosankha zanga.
Ananipatsa zonse; sinidzaiŵala.
Amasamala za umoyo wanga
Nidzatumikila M’lungu kwa umoyo wonse.
2. Mpata ukaoneka wocita zinthu zolakwika.
Na kucoka panjila yabwino yopita kumoyo,
Kukumbukila kudzipeleka kwanga
Inde, kunganilimbitse kwambili.
(KOLASI)
Pa zonse nili nazo pa umoyo wanga,
Coposa zonse, inde capadela
Nikukondweletsa M’lungu mwa zosankha zanga.
Ananipatsa zonse; sinidzaiŵala.
Amasamala za umoyo wanga
Nidzatumikila M’lungu kwa umoyo wonse
(BILIJI)
Moyo wazoona nikonzekela
Bwenzi langa M’lungu adzanithandiza
Moyo weniweni nidzalandila
Ngati Yehova M’lungu Nim’tsangalatsa.
(KOLASI)
Pa zonse nili nazo pa umoyo wanga,
Coposa zonse, inde capadela
Nikukondweletsa M’lungu mwa zosankha zanga.
Ananipatsa zonse; sinidzaiŵala.
Amasamala za umoyo wanga
Nidzatumikila M’lungu kwa umoyo wonse
Nidzatumikila M’lungu kwa umoyo wonse