Limba, Khala na Mphamvu
Daunilodi:
1. Pali mdima panja apa.
Conco apemphela
Za ana ake na za abale
Kuti alimbe mtima.
Zinthu zikavuta
Samabwelela mumbuyo.
Pali nyimbo amakonda
Imamulimbitsa.
(KOLASI)
“N’dzakulimbitsa
Usayope
Nili na iwe,
N’dzakuthandiza,
Iwe limba mtima.”
Akonda Nyimboyi.
“Adzakulimbitsa
Nokupatsa mphamvu.”
(BILIJI)
Nthawi yosakilila
Banja zofunika,
Kaya ziyende bwanji?
Mabwenzi samulekelela, conco,
Iye sadela nkhawa.
2. Adzakalanso na mphamvu,
Monga ni mbalame.
Asamalila zonse za pabanja.
Apemphela ca mumtima.
Ni olema kwambili.
Ayetsetsadi mwamphamvu,
Koma pali nyimbo akonda
Imamulimbitsa.
(KOLASI)
“N’dzakulimbitsa
Usayope
Nili na iwe,
N’dzakuthandiza,
Iwe limba mtima.”
Akonda Nyimboyi.
“Adzakulimbitsa
Nokupatsa mphamvu.
Adzakulimbitsa
Nokupatsa mphamvu.”