Malo Amene Adzakubweletselani Citamando
Daunilodi:
1. Yehova Mulungu Wamphamvu,
Ndimwe munalenga zonse.
Inde, ngakhale kumwambako
Imwe simungakwaneko.
Malowa olambililamo
Ndipo ni otsangalatsa.
Timakondwela capamodzi
Pamene titumikila.
(BILIJI)
Zonse tili nazo
Ndimwe munatipatsa.
Inde, zonse zimene tipeleka n’zanu.
(KOLASI)
Zikomo Atate Yehova
Pa zonse mwaticitila.
Malowa adzabweletsadi
Citamando kwa inuyo.
2. Yehova munali kudziŵa
Zofuna za mtima wathu.
Mwatipatsa malo abwino
Okwezela dzina lanu.
Malowa adzathandizila
Atumiki anu onse
Kuti aigwiledi nchito
Yolalikila kwa onse.
(BILIJI)
Ise tipeleka
Nthawi na cuma cathu
Ndinu woyeneleladi
Kutamandiwa.
(KOLASI)
Zikomo Atate Yehova
Pa zonse mwaticitila.
Malowa adzabweletsadi
Citamando kwa inuyo.