Tikhale Monga Mwana
Daunilodi:
1. Yesu ananena
Tikhale monga ana.
Tikhale monga ana ang’ono,
M’dziko lopanda cikondi.
Tione ena
Monga Mulungu amaŵaonela.
(KOLASI)
Monga mwana,
Tikondane na anzathu,
Tiyese kuona zabwino mwa ena.
Monga mwana,
Tikhale okoma mtima
Tipewe,
Zonse zingatigaŵanitse.
2. Pamene tikukula,
M’dziko lopanda cikondi
Tingayambe kukayikilana,
Muzokamba na m’zocita.
Tiziyesetsa
Kuona ena monga otiposa.
(KOLASI)
Monga mwana,
Tikondane na anzathu,
Tiyese kuona zabwino mwa ena.
Monga mwana,
Tikhale okoma mtima
Tipewe,
Zonse zingatigaŵanitse.
Monga ka mwana.
(BILIJI)
Potumikila,
Yehova M’lungu
M’dziko lonyada,
Tikumbukile,
Tifunikila kukhala na mtima,
Monga cabe
Wa kamwana.
(KOLASI)
Monga mwana,
Tikondane na anzathu,
Tiyese kuona zabwino mwa ena.
Monga mwana,
Tikhale okoma mtima
Tipewe,
Zonse zingatigaŵanitse.
Monga ka mwana..