Misonkhano ya Mpingo ya Mboni za Yehova
Dziŵani zokhudza misonkhano yathu. Pezani malo amene timacitila misonkhano pafupi na kwanu.
Kodi pa misonkhano yathu pamacitika ciani?
A Mboni za Yehova amacita misonkhano kaŵili pa mlungu kuti alambile Mulungu. (Aheberi 10:24, 25) Pa misonkhano imeneyi aliyense angapezekepo ndipo timaphunzila zimene Baibulo limanena ndi mmene tingagwilitsile nchito malangizo ake pa umoyo wathu.
Pa misonkhano imeneyi anthu amakambilana nkhani za m’Baibulo zimene zimacitika monga mmene ana a sukulu amaphunzilila. Misonkhanoyi imayamba ndi kutha ndi nyimbo ndiponso pemphelo.
Simufunikila kukhala wa Mboni za Yehova kuti mupezeke pa misonkhano yathu. Aliyense ndi wolandilidwa ndipo sitilipilisa. Sipakhala kuyendetsedwa mbale ya zopeleka.